-
Maliko 8:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ndiyeno Yesu ndi ophunzira ake anachoka nʼkupita kumidzi ya Kaisareya wa Filipi. Ali mʼnjira, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 28 Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane Mʼbatizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumanena kuti mmodzi wa aneneri.”
-