-
Mateyu 26:47-51Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Mawu adakali mʼkamwa, Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi gulu lalikulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi kwa akulu, atanyamula malupanga ndi zibonga.+
48 Apa nʼkuti womuperekayu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndikamukise ndi yemweyo, mukamugwire.” 49 Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu nʼkunena kuti: “Moni Rabi!” Ndipo anamukisa. 50 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Bwanawe, wabwera kudzatani kuno?”+ Nthawi yomweyo iwo anayandikira ndipo anagwira Yesu nʼkumumanga. 51 Koma mmodzi mwa anthu amene anali ndi Yesu anasolola lupanga lake nʼkutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+
-
-
Luka 22:47-51Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Mawu adakali mʼkamwa, panafika gulu la anthu limodzi ndi Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, akuwatsogolera. Ndiyeno Yudasi anapita pamene panali Yesu kuti akamukise.*+ 48 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa munthu ndi kisi?” 49 Anthu amene anali naye pafupi ataona zimene zinkachitika anati: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?” 50 Mmodzi wa iwo anatemadi kapolo wa mkulu wa ansembe nʼkuduliratu khutu lake lakumanja.+ 51 Koma Yesu anati: “Musachite zimenezi.” Ndipo anagwira khutu lija nʼkumuchiritsa.
-