62 Atamva zimenezo mkulu wa ansembe anaimirira nʼkumufunsa kuti: “Kodi suyankha? Kodi sukumva zimene anthuwa akukunenezazi?”+ 63 Koma Yesu anangokhala chete.+ Choncho mkulu wa ansembe anamuuza kuti: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo, utiuze ngati ndiwedi Khristu, Mwana wa Mulungu!”+