-
Maliko 1:23-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Pa nthawiyo, mʼsunagoge mwawomo munali munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa, ndipo munthuyo anafuula kuti: 24 “Kodi mukufuna chiyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu!”+ 25 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!” 26 Choncho mzimu wonyansawo unamuchititsa kuti aphuphe ndipo unafuula mokweza. Kenako unatuluka mwa munthuyo. 27 Ataona zimenezi, anthu onse anadabwa kwambiri moti anayamba kukambirana kuti: “Kodi chimenechi nʼchiyani? Nʼchiphunzitso chatsopano! Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu ndipo ikumumvera.” 28 Choncho mbiri yake inawanda mofulumira kwambiri mʼchigawo chonse cha Galileya.
-