-
Mateyu 16:13-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Atafika mʼchigawo cha Kaisareya wa Filipi, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndi ndani?”+ 14 Iwo anayankha kuti: “Ena akumanena kuti ndinu Yohane Mʼbatizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumanena kuti Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.” 15 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” 16 Simoni Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu,+ Mwana wa Mulungu wamoyo.”+
-
-
Maliko 8:27-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ndiyeno Yesu ndi ophunzira ake anachoka nʼkupita kumidzi ya Kaisareya wa Filipi. Ali mʼnjira, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 28 Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane Mʼbatizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumanena kuti mmodzi wa aneneri.” 29 Ndiyeno anafunsa ophunzirawo kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu.”+ 30 Atanena zimenezo, anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye.+
-