-
1 Mafumu 10:4-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru zonse za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+ 5 chakudya chapatebulo pake,+ operekera zakumwa, mmene atumiki ake ankakhalira pa nthawi ya chakudya, mmene operekera zakudya ankachitira komanso zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse, inasowa chonena. 6 Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani zimene ndinamva kudziko langa zokhudza zimene mwakwanitsa kuchita komanso nzeru zanu ndi zoona. 7 Koma sindinakhulupirire zimene ndinauzidwa mpaka pamene ndabwera nʼkuona ndi maso anga. Panopa ndaona kuti zimene ndinauzidwa zinali hafu chabe. Nzeru zanu ndi ulemerero wanu zaposa kwambiri zinthu zimene ndinamva.
-