-
Yohane 13:3-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Yesu ankadziwa kuti Atate anapereka zinthu zonse mʼmanja mwake komanso kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndiponso kuti ankapita kwa Mulungu.+ 4 Choncho anaimirira pa chakudya chamadzulocho nʼkuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo nʼkulimanga mʼchiuno mwake.+ 5 Atatero anathira madzi mʼbeseni nʼkuyamba kusambitsa mapazi a ophunzirawo komanso kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga mʼchiuno lija.
-