9 Muzigwira ntchito zanu zonse kwa masiku 6.+ 10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu. Musamagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo amene akukhala mumzinda wanu.+