Machitidwe 17:1, 2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Kenako iwo anayenda kudutsa ku Amfipoli ndi ku Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika,+ kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2 Choncho mwachizolowezi chake,+ Paulo analowa mʼsunagogemo ndipo kwa milungu itatu anakambirana nawo mfundo za mʼMalemba.+ Machitidwe 18:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Paulo ankakamba nkhani mʼsunagoge+ tsiku la sabata lililonse+ ndipo ankakopa Ayuda ndi Agiriki. Machitidwe 19:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kwa miyezi itatu, Paulo ankapita kusunagoge+ kumene ankalankhula molimba mtima. Kumeneko ankakamba nkhani ndiponso kuwafotokozera mfundo zogwira mtima zokhudza Ufumu wa Mulungu.+
17 Kenako iwo anayenda kudutsa ku Amfipoli ndi ku Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika,+ kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2 Choncho mwachizolowezi chake,+ Paulo analowa mʼsunagogemo ndipo kwa milungu itatu anakambirana nawo mfundo za mʼMalemba.+
8 Kwa miyezi itatu, Paulo ankapita kusunagoge+ kumene ankalankhula molimba mtima. Kumeneko ankakamba nkhani ndiponso kuwafotokozera mfundo zogwira mtima zokhudza Ufumu wa Mulungu.+