-
Genesis 3:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako Mulungu anauza Adamu* kuti: “Popeza wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti,+ ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi.+ Udzavutika kulima nthakayo masiku onse a moyo wako+ kuti upeze chakudya. 18 Minga ndi zitsamba zobaya zidzamera panthaka, ndipo chakudya chako chidzakhala zomera zamʼnthaka. 19 Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+
-