-
Machitidwe 15:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Atatsutsana kwambiri za nkhaniyi, Petulo anaimirira nʼkuwauza kuti: “Abale anga, mukudziwa bwino kuti mʼmasiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu, kuti kudzera pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino nʼkukhulupirira.+ 8 Ndipo Mulungu, amene amadziwa zamumtima,+ anachitira umboni powapatsa mzimu woyera+ ngati mmene anachitiranso kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse mʼpangʼono pomwe pakati pa ife ndi iwo.+ Koma anayeretsa mitima yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.+
-