-
1 Akorinto 6:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu?+ Musapusitsidwe.* Achiwerewere,*+ olambira mafano,+ achigololo,+ amuna amene amalola kugonedwa ndi amuna anzawo,+ amuna ogona amuna anzawo,+ 10 akuba, adyera,+ zidakwa,+ olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.+
-
-
Agalatiya 5:19-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Tsopano ntchito za thupi lochimwali zimaonekera mosavuta. Ntchito zimenezi ndi chiwerewere,*+ khalidwe limene limadetsa munthu, khalidwe lopanda manyazi,*+ 20 kulambira mafano, kukhulupirira mizimu,*+ chidani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, 21 kaduka, kumwa mwauchidakwa,*+ maphwando oipa,* ndi zina zotero.+ Abale, mogwirizana ndi zimene ndinakuchenjezani kale, ndikukuchenjezaninso kuti anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.+
-