-
Aheberi 9:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Chifukwa ngati magazi a mbuzi ndi a ngʼombe zamphongo+ komanso phulusa la ngʼombe yaikazi,* zimene amawaza nazo anthu odetsedwa, zimawayeretsa mpaka kukhaladi oyera pamaso pa Mulungu,+ 14 kuli bwanji magazi a Khristu,+ amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu woyera?* Kodi magazi amenewo sadzayeretsa zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika kwa Mulungu wamoyo?+
-
-
1 Petulo 1:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani*+ ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. 19 Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali+ a Khristu,+ omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.+
-