-
Machitidwe 3:5-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Iye anawayangʼanitsitsa, akuyembekeza kuti amupatsa kanthu. 6 Koma Petulo anati: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda!”+ 7 Atatero anamugwira dzanja lamanja nʼkumuimiritsa.+ Nthawi yomweyo mapazi ndi miyendo* yake zinalimba.+ 8 Zitatero anadumpha nʼkuimirira+ ndipo anayamba kuyenda. Iye analowa nawo limodzi mʼkachisimo, akuyenda, kudumphadumpha komanso kutamanda Mulungu.
-