-
Aroma 15:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Abale a ku Makedoniya ndi a ku Akaya apereka mosangalala mphatso kwa oyera ena a ku Yerusalemu omwe ndi osauka.+ 27 Nʼzoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Chifukwa ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti nawonso ayenera kutumikira oyerawo powapatsa zinthu zofunika pa moyo.+
-
-
2 Akorinto 8:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Koma ndikufuna kuti zinthu zambiri zimene muli nazo zithandize pa zimene iwowo alibe, ndipo zambiri zimene iwowo ali nazo zithandize pa zimene inuyo mulibe, kuti pakhale kufanana.
-