-
Aroma 16:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Tsopano ndikukulimbikitsani abale, kuti musamale ndi amene amagawanitsa anthu ndiponso kuchita zinthu zokhumudwitsa ena. Zimenezi ndi zosemphana ndi zimene munaphunzira, choncho muziwapewa.+ 18 Chifukwa anthu oterowo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a mimba zawo. Ndipo amagwiritsa ntchito mawu okopa ndiponso achinyengo kuti apusitse anthu oona mtima.
-
-
2 Petulo 2:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Komabe pakati pa Aisiraeli, anthu ena anakhala aneneri abodza.* Mofanana ndi zimenezi pakati panu padzakhalanso aphunzitsi abodza.*+ Anthu amenewa adzayambitsa mwachinsinsi timagulu towononga tampatuko ndipo adzakana ngakhale Ambuye wawo amene anawagula.+ Chifukwa chochita zimenezi, iwo adzawonongedwa mofulumira kwambiri.
-