-
1 Petulo 1:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Atamandike Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, yemwenso ndi Atate wake. Mulungu anatisonyeza chifundo chachikulu pamene anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano+ nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika.+ Zimenezi zinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+ 4 Anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka.+ Cholowa chimenechi anakusungirani kumwamba.+
-