-
Akolose 2:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Zili choncho chifukwa munaikidwa naye limodzi mʼmanda pobatizidwa ubatizo wofanana ndi wake.+ Ndipo popeza muli naye pa ubwenzi komanso mumakhulupirira zinthu zimene Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa+ anapanga ndi mphamvu zake, munaukitsidwa naye limodzi.+
13 Kuwonjezera pamenepo, ngakhale kuti munali akufa chifukwa cha machimo anu komanso chifukwa choti munali osadulidwa, Mulungu anakupatsani moyo kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu.+ Mokoma mtima anatikhululukira machimo athu onse+
-