9 Koma zokhudza kukonda abale,+ nʼzosafunika kuti tichite kukulemberani chifukwa inuyo, Mulungu amakuphunzitsani kuti muzikondana.+ 10 Ndipotu mukuchita kale zimenezi kwa abale onse ku Makedoniya konse. Koma tikukulimbikitsani abale kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira.