-
1 Timoteyo 6:13-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Pamaso pa Mulungu, amene amathandiza kuti zinthu zonse zikhalebe zamoyo ndiponso pamaso pa Khristu Yesu, amene anapereka umboni wabwino kwambiri pamaso pa Pontiyo Pilato,+ ndikukulamula 14 kuti uzisunga malamulo. Uziwasunga uli woyera ndiponso wopanda chifukwa chokunenezera mpaka pamene Ambuye wathu Yesu Khristu adzaonekere.+ 15 Iye ndi wachimwemwe ndi Wamphamvu komanso ndi Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,+ ndipo adzaonekera pa nthawi yake.
-