-
Aefeso 6:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Muzindipemphereranso ineyo kuti ndikayamba kulankhula ndizipeza mawu oyenerera nʼcholinga choti ndizitha kulankhula molimba mtima ndikamalalikira zokhudza chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino,+ 20 umene ndine kazembe+ wake womangidwa ndi unyolo ndiponso kuti ndilankhule za uthengawo molimba mtima ngati mmene ndikuyenera kuchitira.
-
-
Afilipi 1:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Nʼzoyenera kwa ine kuti ndiganizire nonsenu mwa njira imeneyi, chifukwa ndinu apamtima panga. Inu amene munandithandiza pa nthawi imene ndinamangidwa maunyolo mʼndende+ komanso poteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito yolengeza uthenga wabwino.+ Inu limodzi ndi ine tinapindula ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.
-