-
Danieli 3:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Koma amuna atatuwa, Shadireki, Misheki ndi Abedinego, anagwera mungʼanjo ya motoyo ali omangidwa.
24 Ndiyeno Mfumu Nebukadinezara inachita mantha kwambiri ndipo inanyamuka mwachangu nʼkufunsa nduna zake zapamwamba kuti: “Kodi sitinaponye amuna atatu pamoto titawamanga?” Ndunazo zinayankha mfumuyo kuti: “Inde, mfumu.” 25 Ndiyeno mfumu inati: “Taonani! Inetu ndikuona amuna 4 akuyendayenda pakati pa moto ali osamangidwa komanso sakupsa, ndipo munthu wa 4 akuoneka ngati mwana wa milungu.”
-