Yesaya 53:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Koma iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+ Analandira chilango kuti ife tikhale pamtendere,+Ndipo chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa.+ Aroma 3:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Mulungu anamupereka ngati nsembe yoti anthu agwirizanenso ndi Mulunguyo+ pokhulupirira magazi ake.+ Anachita zimenezi pofuna kuonetsa chilungamo chake chifukwa anasonyeza kuti ndi wosakwiya msanga pokhululuka machimo amene anachitika kale. 1 Timoteyo 1:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona komanso oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. Pa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+ Aheberi 2:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Choncho iye anayenera kukhala ngati “abale” ake pa zinthu zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo komanso wokhulupirika pa zinthu zokhudza Mulungu, nʼcholinga choti apereke nsembe yophimba machimo a anthu+ kuti tigwirizanenso ndi Mulungu. 1 Petulo 2:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Iye ananyamula machimo athu+ mʼthupi lake pamene anamukhomerera pamtengo.+ Anachita zimenezi kuti tipulumutsidwe ku uchimo nʼkumachita zinthu zolungama. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+ 1 Yohane 4:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Mulungu anatumiza Mwana wake monga nsembe yophimba+ machimo athu.*+ Anachita zimenezi chifukwa chakuti anatikonda, osati chifukwa choti ifeyo ndi amene tinamukonda.
5 Koma iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+ Analandira chilango kuti ife tikhale pamtendere,+Ndipo chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa.+
25 Mulungu anamupereka ngati nsembe yoti anthu agwirizanenso ndi Mulunguyo+ pokhulupirira magazi ake.+ Anachita zimenezi pofuna kuonetsa chilungamo chake chifukwa anasonyeza kuti ndi wosakwiya msanga pokhululuka machimo amene anachitika kale.
15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona komanso oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. Pa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+
17 Choncho iye anayenera kukhala ngati “abale” ake pa zinthu zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo komanso wokhulupirika pa zinthu zokhudza Mulungu, nʼcholinga choti apereke nsembe yophimba machimo a anthu+ kuti tigwirizanenso ndi Mulungu.
24 Iye ananyamula machimo athu+ mʼthupi lake pamene anamukhomerera pamtengo.+ Anachita zimenezi kuti tipulumutsidwe ku uchimo nʼkumachita zinthu zolungama. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+
10 Mulungu anatumiza Mwana wake monga nsembe yophimba+ machimo athu.*+ Anachita zimenezi chifukwa chakuti anatikonda, osati chifukwa choti ifeyo ndi amene tinamukonda.