-
Aheberi 6:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Pali anthu amene Mulungu anawaunikira,+ amene analandirapo mphatso yaulere yakumwamba, amene analandira mzimu woyera 5 komanso amene anamvapo mawu abwino a Mulungu ndi madalitso* amene adzaperekedwe padziko limene likubweralo. 6 Koma tsopano anthu amenewa anagwa+ ndipo nʼzosatheka kuwadzutsanso kuti alape, chifukwa akupachika kachiwiri Mwana wa Mulungu ndiponso kumunyoza poyera.+
-