Ezara
4 Adani a Yuda ndi Benjamini+ atamva kuti anthu amene anabwera kuchokera ku ukapolo+ akumangira kachisi Yehova Mulungu wa Isiraeli, 2 nthawi yomweyo anapita kwa Zerubabele ndi atsogoleri a nyumba za makolo nʼkukawauza kuti: “Bwanji tizimanga limodzi chifukwa ifeyo, mofanana ndi inuyo, timalambira* Mulungu wanu.+ Komanso timapereka nsembe kwa iye kuyambira mʼmasiku a Esari-hadoni+ mfumu ya Asuri, yemwe anatibweretsa kuno.”+ 3 Koma Zerubabele, Yesuwa ndi atsogoleri ena onse a nyumba za makolo za Isiraeli anawayankha kuti: “Sizingatheke kuti timange nyumba ya Mulungu wathu limodzi ndi inu.+ Timanga tokha nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, mogwirizana ndi zimene Mfumu Koresi ya Perisiya yatilamula.”+
4 Kuyambira nthawi imeneyo, anthu amʼdzikolo anayamba kufooketsa* anthu a ku Yuda komanso kuwagwetsa ulesi kuti asapitirize ntchito yomanga.+ 5 Komanso, analemba ntchito alangizi kuti asokoneze mapulani awo+ pa nthawi yonse imene Koresi mfumu ya Perisiya ankalamulira, mpaka mu ulamuliro wa Dariyo+ mfumu ya Perisiya. 6 Kumayambiriro kwa ulamuliro wa Ahasiwero, iwo analemba kalata yonena zoipa zokhudza anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu. 7 Mʼmasiku a Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzake ena onse analembera kalata mfumuyo. Kalatayo anaimasulira mʼChiaramu+ nʼkuilemba mʼzilembo za Chiaramu.*
8 * Rehumu mtsogoleri wa akuluakulu a boma ndi Simusai mlembi, analemba kalata yopita kwa mfumu Aritasasita yonena zoipa za anthu a ku Yerusalemu. Analemba kuti: 9 (Inachokera kwa Rehumu mtsogoleri wa akuluakulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse monga oweruza ndi abwanamkubwa aangʼono, alembi ena, anthu a ku Ereke,+ Ababulo, anthu a ku Susa,+ kapena kuti Aelamu,+ 10 mitundu ina yonse imene Asinapera wamkulu ndi wolemekezeka anaitenga kupita nayo ku ukapolo nʼkukaiika mʼmizinda ya ku Samariya+ ndi ena onse akutsidya lina la Mtsinje* . . . Tsopano 11 izi nʼzimene analemba mʼkalata imene anatumizayo.)
“Kwa mfumu Aritasasita, kuchokera kwa ife akapolo anu, amuna akutsidya lina la Mtsinje: Tsopano 12 inu mfumu dziwani kuti Ayuda amene anachokera kwa inu nʼkubwera kuno afika ku Yerusalemu. Iwo akumanganso mzinda woukira ndiponso woipa uja. Akumanganso mpanda+ komanso kukonza maziko. 13 Ndiyeno inu mfumu dziwani kuti, mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake nʼkumalizidwa, anthu amenewa asiya kupereka msonkho umene munthu aliyense amapereka, msonkho wakatundu+ ndi msonkho wamsewu ndipo zimenezi zidzachititsa kuti chuma cha mafumu chiwonongeke. 14 Tsopano popeza ife timalandira malipiro ochokera kunyumba yachifumu,* si bwino kuti tingolekerera kuti inu mfumu chuma chanu chiwonongeke. Choncho, tatumiza kalatayi kuti tikudziwitseni zimenezi inu mfumu 15 nʼcholinga choti mufufuze mʼbuku la mbiri ya makolo anu.+ Mukafufuza mʼbukulo mupeza kuti umenewu ndi mzinda woukira mafumu ndi zigawo za mayiko. Mumzinda umenewu mwakhala muli anthu oyambitsa kugalukira kuyambira kalekale. Nʼchifukwa chake mzindawu unawonongedwa.+ 16 Tikukudziwitsani mfumu kuti mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake nʼkumalizidwa, simudzalamuliranso kutsidya lino la Mtsinje.”+
17 Ndiyeno mfumuyo inatumiza uthenga kwa Rehumu mtsogoleri wa akuluakulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse amene ankakhala ku Samariya ndiponso kwa ena onse omwe ankakhala kutsidya lina la Mtsinje. Uthengawo unali wakuti:
“Moni! 18 Kalata imene mwatitumizira yawerengedwa* momveka bwino pamaso panga. 19 Choncho ine ndinalamula kuti afufuze, ndipo apeza kuti kuyambira kale mzinda umenewo wakhala ukuukira mafumu. Anthu amumzindawo akhala akuyambitsanso chisokonezo komanso kugalukira.+ 20 Mafumu amphamvu olamulira Yerusalemu ndi dera lonse la kutsidya lina la Mtsinje ankapatsidwa msonkho umene munthu aliyense amapereka, msonkho wakatundu komanso msonkho wamsewu. 21 Tsopano khazikitsani lamulo loti anthu amenewa asiye ntchitoyo kuti mzindawo usamangidwenso mpaka ine ndidzalamule. 22 Muonetsetse kuti musanyalanyaze kuchita zimenezi kuti vuto limeneli lisakule nʼkuwonongetsa chuma cha mfumu.”+
23 Mawu amene analembedwa mʼkalata ya mfumu Aritasasita anawerengedwa pamaso pa Rehumu, Simusai mlembi ndi anzawo. Kenako iwo anapita msangamsanga kwa Ayuda ku Yerusalemu nʼkukawaletsa ntchitoyo mwankhondo. 24 Pa nthawi imeneyi mʼpamene ntchito yomanga nyumba ya Mulungu, imene inali ku Yerusalemu, inaima ndipo inaima choncho mpaka chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya Perisiya.+