Nyimbo ya Solomo
Ndinamufunafuna koma sindinamupeze.+
2 Choncho ndinati: ‘Ndidzuka nʼkukazungulira mumzinda,
Mʼmisewu ndi mʼmabwalo amumzinda,
Kuti ndikafunefune munthu amene ndimamukonda.’
Ndinamufunafuna koma sindinamupeze.
3 Alonda amene ankazungulira mumzindawo anandipeza.+
Ndipo ine ndinawafunsa kuti: ‘Kodi mwamuonako munthu amene ndimamukonda?’
4 Nditangowapitirira pangʼono,
ndinamʼpeza munthu amene ndimamukonda.
Ndinamugwira ndipo sindinafune kumʼsiya
Mpaka nditamubweretsa mʼnyumba ya mayi anga,+
Mʼchipinda chamkati cha mayi amene anali ndi pakati kuti ine ndibadwe.
5 Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu,
Pali insa ndiponso pali mphoyo zakutchire kuti:
Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.”+
6 “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi nʼchiyani, chooneka ngati utsi wokwera mʼmwamba,
Chonunkhira mafuta a mule ndi lubani,*
Komanso ndi zonunkhira zonse za ufa za munthu wamalonda?”+
7 “Taonani! Ndi bedi la Solomo.
Lazunguliridwa ndi amuna 60 amphamvu,
Ochokera mwa amuna amphamvu a mu Isiraeli,+
8 Onsewo atenga malupanga,
Ndipo onse ndi ophunzitsidwa nkhondo,
Aliyense wamangirira lupanga lake mʼchiuno
Kuti adziteteze ku zinthu zoopsa za usiku.”
10 Zipilala zake ndi zasiliva,
Motsamira mwake ndi mwagolide.
Chokhalira chake ndi chopangidwa ndi ubweya wa nkhosa wapepo.
Mkati mwake, ana aakazi a ku Yerusalemu
Anakongoletsamo posonyeza chikondi.”