Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto
10 Tsopano ineyo Paulo, ndikukudandaulirani motsanzira Khristu amene ndi wofatsa ndiponso wokoma mtima,+ ngakhale kuti ndimaoneka wofooka ndikakhala pakati panu,+ koma wolimba mtima ndikamalankhula nanu ndili kwina.+ 2 Ndikanakonda kuti ndikadzabwera kumeneko ndisadzachite zinthu zazikulu zimene ndikuyembekezera kudzachita potsutsana ndi anthu ena amene akuona kuti ifeyo tinachita zinthu ngati anthu amʼdzikoli.* 3 Ngakhale kuti moyo wathu ndi wofanana ndi wa anthu ena onse, sitikumenya nkhondo motsatira maganizo amʼdzikoli. 4 Zida zimene tikumenyera nkhondoyi si zamʼdzikoli,+ koma ndi zida zamphamvu zimene Mulungu+ watipatsa ndipo zimatha kugwetsa zinthu zozikika molimba. 5 Chifukwa tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu,+ ndipo tikugonjetsa maganizo alionse nʼkuwamanga ngati mkaidi kuti azimvera Khristu. 6 Komanso ndife okonzeka kupereka chilango kwa munthu aliyense wosamvera,+ inuyo mukadzasonyeza kuti ndinu omvera pa chilichonse.
7 Mukuona zinthu potengera maonekedwe akunja. Ngati aliyense amakhulupirira mumtima mwake kuti ndi wotsatira Khristu, aganizirenso kuti: Mmene zilili kuti iyeyo amatsatira Khristu, ifenso timatsatira Khristu. 8 Ambuye anatipatsa ulamuliro kuti tikulimbikitseni, osati kukufooketsani. Ndipo nditati ndidzitamandire mopitirirako malire zokhudza ulamulirowu,+ sindingachite manyazi. 9 Chifukwa sindikufuna kuti muganize kuti cholinga cha makalata anga nʼkukuopsezani. 10 Popeza ena amati: “Makalata ake amakhala ndi uthenga wamphamvu, koma iyeyo akabwera amaoneka wofooka ndipo zolankhula zake zimakhala zosagwira mtima.” 11 Anthu amenewo adziwe kuti zimene tikunena mʼmakalata athu tili kwina, tidzachitanso zomwezo tikadzabwera.+ 12 Sitidziona ngati ndife ofanana ndi anthu amene amadzikweza komanso sitidziyerekezera ndi anthuwo.+ Koma anthu amenewo akamayezana okhaokha pogwiritsa ntchito mfundo zawo nʼkumadziyerekezera okhaokha, samvetsa chilichonse.+
13 Koma ifeyo sitidzadzitamandira pa zinthu zimene zili kunja kwa malire amene tapatsidwa. Tidzadzitamandira pa zinthu zimene zili mkati mwa malire a gawo limene Mulungu watiyezera, limene linafika mpaka kwanuko.+ 14 Choncho sitikupitirira malire a gawo lathu, ngati kuti gawolo silikufika kwanuko. Chifukwa tinayamba ndife kufika kwanuko polengeza uthenga wabwino wonena za Khristu.+ 15 Sikutinso tikudzitamandira kunja kwa malire a gawo limene tinapatsidwa chifukwa cha ntchito ya munthu wina. Koma tikukhulupirira kuti chikhulupiriro chanu chikadzawonjezeka, ntchito yathunso idzakula mʼgawo lathu. Ndiyeno tidzakhala ndi zochita zambiri 16 nʼcholinga choti tilengeze uthenga wabwino kumayiko akutali kupitirira kwanuko, kuti tisadzitamande pa ntchito imene yagwiridwa kale mʼgawo la munthu wina. 17 “Koma amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”*+ 18 Chifukwa amene amavomerezedwa si wodzikweza,+ koma amene Yehova* wamuvomereza.+