Ezara
6 Pa nthawiyi mʼpamene mfumu Dariyo inaika lamulo loti afufuze mʼnyumba yosungiramo zinthu zakale, momwe ankasungamonso zinthu zamtengo wapatali zimene zinapititsidwa ku Babulo. 2 Kumalo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri a ku Ekibatana, mʼchigawo cha dziko la Amedi, anapezako mpukutu. Mumpukutuwo munalembedwa uthenga wakuti:
3 “Mʼchaka choyamba cha Mfumu Koresi, mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti:+ ‘Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe kumeneko ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo ikhale mikono 60* kupita mʼmwamba ndiponso mikono 60 mulifupi mwake.+ 4 Ikhale ndi mizere itatu yamiyala ikuluikulu yochita kugubuduza komanso mzere umodzi wa matabwa.+ Ndalama zake zichokere kunyumba ya mfumu.+ 5 Ziwiya zagolide ndi zasiliva za mʼnyumba ya Mulungu, zimene Nebukadinezara anatenga mʼkachisi yemwe anali ku Yerusalemu nʼkuzipititsa ku Babulo,+ zibwezedwe kuti zikaikidwe kumalo ake, kukachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo zikaikidwe mʼnyumba ya Mulungu.’+
6 Tsopano inu Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,* Setara-bozenai ndi anzanu ndiponso abwanamkubwa aangʼono amene ali kutsidya lina la Mtsinje,+ musapite kumeneko. 7 Musakasokoneze ntchito yomanga nyumba ya Mulungu. Bwanamkubwa wa Ayuda ndi akuluakulu a Ayuda amanganso nyumba ya Mulunguyo pamalo ake. 8 Ndaikanso lamulo lokhudza zimene muyenera kuchita ndi akuluakulu a Ayuda amenewa pa ntchito yomanganso nyumba ya Mulungu. Amuna amenewa muziwapatsa ndalama zochokera pa chuma cha mfumu+ zomwe anthu a kutsidya la Mtsinje amapereka pokhoma msonkho kuti ntchitoyo isaime.+ 9 Komanso muziwapatsa zinthu zomwe akufunikira monga ngʼombe zingʼonozingʼono zamphongo,+ nkhosa zamphongo+ ndi ana a nkhosa+ kuti azipereka nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba. Muziwapatsanso tirigu,+ mchere,+ vinyo+ ndi mafuta+ mogwirizana ndi zimene ansembe amene ali ku Yerusalemu anganene. Muziwapatsa zinthu zimenezi tsiku ndi tsiku 10 kuti nthawi zonse azipereka nsembe zosangalatsa Mulungu wakumwamba ndiponso kuti azipempherera mfumu ndi ana ake kuti akhale ndi moyo wabwino.+ 11 Ndaikanso lamulo lakuti aliyense wophwanya lamulo limeneli, thabwa* lidzachotsedwe panyumba yake ndipo iye adzapachikidwe pathabwalo. Komanso nyumba yake idzasandutsidwa chimbudzi* cha aliyense chifukwa cha zimenezi. 12 Mulungu amene anaika dzina lake kumeneko,+ achotse mfumu iliyonse ndi anthu alionse ophwanya lamulo limeneli ndiponso owononga nyumba ya Mulungu imene ili ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndaika lamulo limeneli, ndipo zichitike mwamsanga.”
13 Kenako Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje, Setara-bozenai+ ndi anzawo anachita zimenezi mwamsanga mogwirizana ndi mawu amene mfumu Dariyo inatumiza. 14 Tsopano akuluakulu a Ayuda anapitiriza kumanga ndipo ntchitoyo inkayenda bwino+ chifukwa cholimbikitsidwa ndi ulosi wa mneneri Hagai+ ndi Zekariya+ mdzukulu wa Ido. Iwo anamanga nyumbayo nʼkuimaliza potsatira lamulo la Mulungu wa Isiraeli+ ndi lamulo la Koresi,+ Dariyo+ komanso Aritasasita mfumu ya Perisiya.+ 15 Iwo anamaliza nyumbayo pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara,* mʼchaka cha 6 cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo.
16 Ndiyeno Aisiraeli, ansembe, Alevi+ ndi anthu ena onse amene anachokera ku ukapolo, anatsegulira nyumba ya Mulunguyo mosangalala. 17 Iwo anapereka nsembe ngʼombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200 ndi ana a nkhosa amphongo 400. Anaperekanso mbuzi zamphongo 12 za nsembe yamachimo ya Aisiraeli onse, mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Isiraeli.+ 18 Kenako anaika ansembe ndi Alevi mʼmagulu awo kuti azitumikira Mulungu ku Yerusalemu+ mogwirizana ndi malangizo a mʼbuku la Mose.+
19 Anthu amene anachokera ku ukapolowo anachita Pasika pa tsiku la 14 la mwezi woyamba.+ 20 Chifukwa chakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ ndipo palibe anatsala, onse anali oyera. Choncho Aleviwo anapha nyama ya Pasika ya anthu onse amene anachokera ku ukapolo, ya abale awo ansembe ndiponso yawo. 21 Ndiyeno Aisiraeli amene anabwera kuchokera ku ukapolo anadya nyamayo. Komanso aliyense amene anadzilekanitsa ku zonyansa za anthu a mitundu yamʼdzikolo nʼkubwera kwa iwo kuti alambire* Yehova Mulungu wa Isiraeli, anadya nawo.+ 22 Kwa masiku 7, iwo anachita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa+ mosangalala chifukwa Yehova anawachititsa kuti asangalale. Iye anachititsa kuti mfumu ya Asuri iwakomere mtima+ nʼkuwathandiza* pa ntchito yomanga nyumba ya Mulungu woona, Mulungu wa Isiraeli.