Yesaya
16 Tumizani nkhosa yamphongo kwa wolamulira wa dziko,
Kuchokera ku Sela kudutsa kuchipululu
Kukafika kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.*
2 Pamalo owolokera chigwa cha Arinoni,+
Ana aakazi a Mowabu adzakhala ngati mbalame yomwe yathamangitsidwa pachisa chake.+
3 “Perekani malangizo, chitani zimene zagamulidwa.
Chititsani kuti masana, mthunzi wanu ukhale waukulu ndipo uchititse mdima ngati wa usiku.
Bisani anthu amene abalalitsidwa ndipo amene akuthawa musawapereke kwa adani awo.
4 Anthu anga amene abalalitsidwa akhale mʼdziko lako, iwe Mowabu.
Iwe ukhale malo awo obisalamo pamene akuthawa wowononga.+
Wopondereza adzafika pamapeto ake,
Chiwonongeko chidzatha,
Ndipo amene akupondaponda anzawo adzatha padziko lapansi.
5 Kenako mpando wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chikondi chokhulupirika.
Amene adzakhale pampandowo mutenti ya Davide adzakhala wokhulupirika.+
Iye adzaweruza mwachilungamo, ndipo adzachita mwachangu zinthu zachilungamo.”+
6 Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, iye ndi wonyada kwambiri.+
Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake ndi mkwiyo wake.+
Koma zolankhula zake zopanda pake sizidzachitika.
7 Choncho Mowabu adzalira mofuula chifukwa cha tsoka lake.
Aliyense wokhala mʼMowabu adzalira mofuula.+
Omenyedwawo adzalirira mphesa zouma zoumba pamodzi za ku Kiri-hareseti.+
8 Chifukwa minda yamʼmapiri ya ku Hesiboni+ yafota,
Chimodzimodzinso mitengo ya mpesa ya ku Sibima,+
Olamulira anthu a mitundu ina apondaponda nthambi zake zofiira kwambiri.*
Nthambizo zinafika mpaka ku Yazeri,+
Zinafika mpaka kuchipululu.
Mphukira zake zinakula mpaka zinafika kunyanja.
9 Nʼchifukwa chake ndidzalirire mtengo wa mpesa wa ku Sibima pamene ndikulirira Yazeri.
Ndidzakunyowetsa kwambiri ndi misozi yanga iwe Hesiboni ndi Eleyale,+
Chifukwa chakuti kufuula kosangalalira zipatso zamʼchilimwe komanso zokolola zako kwatha.*
10 Kukondwera ndi kusangalala zachotsedwa mʼmunda wako wazipatso,
Ndipo mʼminda ya mpesa simukumveka nyimbo zachisangalalo kapena kufuula.+
Oponda mphesa sakupondanso mphesa kuti apange vinyo,
Chifukwa ndachititsa kuti kufuula kulekeke.+
11 Nʼchifukwa chake mkati mwanga mukunjenjemera chifukwa cha Mowabu,+
Mukunjenjemera ngati zingwe za zeze,
Ndipo mʼmimba mwanga mukunjenjemera chifukwa cha Kiri-hareseti.+
12 Ngakhale Mowabu atadzitopetsa pamalo okwezeka nʼkupita kukapemphera kumalo ake opatulika, sadzapindula chilichonse.+
13 Awa ndi mawu okhudza Mowabu amene Yehova ananena mʼmbuyomu. 14 Koma tsopano Yehova wanena kuti: “Pomatha zaka zitatu, mofanana ndi zaka za munthu waganyu,* ulemerero wa Mowabu udzatha. Iye adzachititsidwa manyazi ndipo adzakumana ndi chipwirikiti chamtundu uliwonse ndipo anthu amene adzatsale adzakhala ochepa kwambiri ndiponso opanda mphamvu.”+