Yesaya
30 Yehova wanena kuti: “Tsoka kwa ana aamuna osamvera,+
Amene amachita zofuna zawo osati zofuna zanga,+
Amene amapanga mgwirizano* koma osati motsogoleredwa ndi mzimu wanga,
Kuti awonjezere tchimo pa tchimo.
2 Iwo amapita ku Iguputo+ asanandifunse,+
Kuti akapeze chitetezo kwa Farao*
Ndiponso kuti akabisale mumthunzi wa Iguputo.
3 Koma chitetezo cha Farao chidzakhala chochititsa manyazi kwa inu,
Ndipo kubisala mumthunzi wa Iguputo kudzachititsa kuti munyozeke.+
5 Iwo adzachititsidwa manyazi
Ndi anthu amene sangawathandize chilichonse,
Opanda phindu kapena ubwino uliwonse,
Omwe ndi ochititsa manyazi ndi onyozetsa.”+
6 Uwu ndi uthenga wokhudza zilombo zokhala kumʼmwera:
Podutsa mʼdziko la mavuto ndi la zowawa,
La mkango, mkango umene ukubangula,
La mphiri ndi la njoka zouluka zaululu wamoto,*
Iwo anyamula chuma chawo pamsana pa abulu
Ndiponso katundu wawo pamalinunda a ngamila.
Koma anthuwo sadzapindula ndi zinthu zimenezi.
7 Chifukwa thandizo lochokera ku Iguputo ndi losathandiza ngakhale pangʼono.+
Choncho iye ndamutchula kuti: “Rahabi+ amene amangokhala osachita chilichonse.”
8 “Tsopano pita ukalembe zimenezi pacholembapo, iwo akuona.
Ndipo ukazilembe mʼbuku+
Kuti mʼtsogolo
Zidzakhale umboni mpaka kalekale.+
10 Iwo auza anthu oona masomphenya kuti, ‘Lekani kuona masomphenya,’
Ndipo anthu olosera zamʼtsogolo awauza kuti, ‘Musatiuze masomphenya olondola.+
Mutiuze zinthu zotikomera. Muziona masomphenya abodza.+
11 Patukani panjira. Dzerani njira ina.
Musatiuzenso za Woyera wa Isiraeli.’”+
12 Choncho Woyera wa Isiraeli wanena kuti:
“Chifukwa chakuti mwakana mawu awa,+
Mukudalira katangale komanso chinyengo
Ndipo mukukhulupirira zinthu zimenezi,+
13 Cholakwa chanuchi chidzakhala ngati mpanda wogumuka kwa inu,
Ngati mpanda wautali umene wapendekeka ndipo watsala pangʼono kugwa.
Udzagwa mwadzidzidzi mʼkanthawi kochepa.
14 Udzaphwanyika ngati mtsuko waukulu wadothi,
Udzaphwanyikiratu wonse nʼkungokhala tizidutswatizidutswa ndipo patizidutswapo sipadzapezeka ngakhale phale
Loti nʼkupalira moto
Kapena kutungira madzi pachithaphwi.”*
15 Chifukwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Woyera wa Isiraeli, wanena kuti:
“Mukabwerera kwa ine nʼkukhala odekha, mudzapulumuka.
Mudzakhala amphamvu mukakhala odekha komanso mukasonyeza kuti mukundidalira.”+
Koma inu simunafune.+
16 Mʼmalomwake munanena kuti: “Ayi, ife tidzakwera mahatchi nʼkuthawa!”
Choncho mudzathawadi.
Munanenanso kuti: “Tidzakwera mahatchi othamanga kwambiri!”+
Choncho anthu amene adzakuthamangitseni adzakhala aliwiro kwambiri.+
17 Anthu 1,000 adzanjenjemera chifukwa choopsezedwa ndi munthu mmodzi.+
Mudzathawa chifukwa choopsezedwa ndi anthu 5
Moti ochepa amene adzatsale adzakhala ngati mtengo wautali wapangalawa wozikidwa pamwamba pa phiri,
Adzakhala ngati mtengo wachizindikiro wozikidwa paphiri lalingʼono.+
18 Koma Yehova akuyembekezera moleza mtima kuti akukomereni mtima,+
Ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo,+
Chifukwa Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo.+
Osangalala ndi anthu onse amene akumuyembekezera.+
19 Anthu akadzayamba kukhala ku Ziyoni, ku Yerusalemu,+ inu simudzaliranso.+ Mulungu adzakukomerani mtima akadzamva kulira kwanu kopempha thandizo. Akadzangomva kulira kwanu, nthawi yomweyo adzakuyankhani.+ 20 Ngakhale kuti Yehova adzakupatsani mavuto kuti akhale chakudya chanu ndi kuponderezedwa kuti kukhale madzi anu akumwa,+ Mlangizi wanu wamkulu adzasiya kudzibisa ndipo maso anu adzaona Mlangizi wanu wamkulu.+ 21 Makutu anu adzamva mawu kumbuyo kwanu akuti, “Njira ndi iyi.+ Yendani mʼnjira imeneyi,” kuti musasochere nʼkulowera kudzanja lamanja kapena lamanzere.+
22 Siliva amene munakutira mafano anu ogoba komanso golide amene munakutira mafano anu achitsulo,*+ mudzamuchititsa kuti akhale wonyansa. Mudzamutaya ngati mmene mkazi amene akusamba amatayira kansalu kake, ndipo mudzanena kuti: “Nyansi zimenezi!”+ 23 Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munadzala munthaka,+ ndipo chakudya chochokera munthakayo chidzakhala chochuluka komanso chopatsa thanzi.*+ Pa tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+ 24 Ngʼombe ndi abulu amene analima mundawo, zidzadya chakudya chokoma chosakaniza ndi zitsamba zowawasira, chimene mankhusu ake anauluzidwa pogwiritsa ntchito fosholo ndi chifoloko. 25 Pa tsiku limene anthu ambiri adzaphedwe ndiponso nsanja zidzagwe, paphiri lililonse lalitali ndi paphiri lililonse lalingʼono padzakhala timitsinje ndi ngalande zamadzi.+ 26 Kuwala kwa mwezi wathunthu kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa. Ndipo kuwala kwa dzuwa kudzakhala kwamphamvu kwambiri kuwonjezeka maulendo 7,+ ngati kuwala kwa masiku 7. Zimenezi zidzachitika pa tsiku limene Yehova adzamange mabala* a anthu ake+ amene anavulala ndi kuchiritsa mabala aakulu amene anavulala pamene ankawalanga.+
27 Taonani! Dzina la Yehova likubwera kuchokera kutali.
Likubwera ndi mkwiyo wake woyaka moto ndiponso mitambo yolemera.
Iye akulankhula mwaukali,
Ndipo lilime lake lili ngati moto wowononga.+
28 Mzimu* wa Mulungu uli ngati mtsinje wosefukira umene wafika mʼkhosi,
Kuti agwedeze mitundu ya anthu musefa wachiwonongeko.*
Ndipo pakamwa pa mitundu ya anthuwo padzamangidwa zingwe ngati zowongolera hatchi,+ zimene zidzawachititse kuti asochere.
29 Koma mudzaimba nyimbo ngati imene imaimbidwa usiku
Mukamakonzekera* chikondwerero,+
Ndipo mudzasangalala mumtima mwanu ngati munthu
Amene akuyenda, kwinaku akuimba* chitoliro
Popita kuphiri la Yehova, Thanthwe la Isiraeli.+
30 Yehova adzapangitsa kuti mawu ake aulemerero+ amveke
Ndipo adzapangitsa kuti dzanja lake+ limene likutsika ndi mkwiyo waukulu lionekere.+
Dzanjalo lidzatsika ndi moto wowononga,+
31 Chifukwa cha mawu a Yehova, dziko la Asuri lidzagwidwa ndi mantha,+
Ndipo iye adzalimenya ndi ndodo.+
32 Ulendo uliwonse umene Yehova adzakwapule Asuri
Ndi ndodo yake yoperekera chilango,
Kudzamveka kulira kwa maseche ndi azeze+
Pamene akukweza dzanja lake kuti awalange pankhondo.+
Malo amene iye wakonzawo ndi aakulu komanso ozama
Ndipo kuli moto waukulu ndi nkhuni zambiri.
Mpweya wa Yehova, womwe uli ngati mtsinje wa sulufule,
Udzayatsa malowo.