Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto
2 Choncho abale, pamene ndinabwera kwa inu kudzalengeza za chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu, sindinkalankhula mokokomeza+ kapena mosonyeza kuti ndili ndi nzeru zodabwitsa. 2 Popeza ndinasankha kuti pamene ndili ndi inu ndisadziwe china chilichonse kupatulapo Yesu Khristu, amene anapachikidwa.+ 3 Pamene ndinkabwera kwa inu ndinali wofooka ndipo ndinkanjenjemera ndi mantha. 4 Polankhula ndiponso polalikira, mawu anga sanali okopa kapena osonyeza nzeru, koma oonetsa mzimu ndi mphamvu,+ 5 kuti musamakhulupirire nzeru za anthu koma mphamvu ya Mulungu.
6 Tsopano tikulankhula zokhudza nzeru kwa anthu olimba mwauzimu,+ koma osati nzeru za nthawi* ino kapena za olamulira a nthawi ino amene adzawonongedwa.+ 7 Koma tikunena za nzeru ya Mulungu yomwe ndi nzeru yobisika, imene inaonekera mu chinsinsi chopatulika.+ Mulungu anakonzeratu zimenezi kalekale, kuti tikhale ndi ulemerero. 8 Palibe wolamulira aliyense wa nthawi* ino amene ankadziwa nzeru imeneyi,+ chifukwa akanakhala kuti akuidziwa sakanapha Ambuye waulemerero. 9 Koma mogwirizana ndi zimene Malemba amanena: “Palibe munthu amene anaonapo kapena kumva kapenanso kuganiza zimene Mulungu wakonzera anthu amene amamukonda.”+ 10 Mulungu anatiululira ifeyo zinthu zimenezi+ kudzera mwa mzimu wake,+ chifukwa mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.+
11 Kodi ndi munthu uti amene angadziwe maganizo a munthu wina? Aliyense amangodziwa zimene zili mumtima mwake basi. Mofanana ndi zimenezi, palibe amene akudziwa maganizo a Mulungu, kupatulapo mzimu wa Mulungu. 12 Ife sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu,+ kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima. 13 Timalankhulanso zinthu zimenezi, osati ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu,+ koma ndi mawu amene mzimu watiphunzitsa,+ pamene tikufotokoza zinthu zauzimu ndi mawu auzimu.
14 Koma munthu wokonda zinthu zamʼdziko* savomereza* zinthu za mzimu wa Mulungu, chifukwa amaziona ngati zopusa ndipo sangathe kuzidziwa, chifukwa zimafuna kuzifufuza mwauzimu. 15 Komano munthu wauzimu amafufuza zinthu zonse,+ koma iye safufuzidwa ndi munthu aliyense. 16 Nanga “ndani akudziwa maganizo a Yehova* kuti amulangize?”+ Koma ife tili ndi maganizo a Khristu.+