Oweruza
14 Kenako Samisoni anapita ku Timuna ndipo kumeneko anaona mkazi wa Chifilisiti. 2 Choncho anakauza bambo ndi mayi ake kuti: “Ndaona mkazi wa Chifilisiti wokongola ku Timuna, ndiye mukanditengere kuti akhale mkazi wanga.” 3 Koma bambo ndi mayi akewo anamʼfunsa kuti: “Kodi sungapeze mkazi pakati pa abale ako kapena pakati pa anthu onse a mtundu wathu?+ Zoona mpaka ukatenge mkazi kwa Afilisiti osadulidwa?” Koma Samisoni anauza bambo akewo kuti: “Ingopitani mukanditengere mkazi ameneyu, chifukwa ndiye woyenera kwa ine.”* 4 Bambo ndi mayi akewo sanadziwe kuti Yehova ndi amene ankachititsa zimenezi chifukwa iye* ankafunafuna mpata woti alange Afilisiti, omwe pa nthawiyi ankalamulira Isiraeli.+
5 Choncho Samisoni anapita ku Timuna pamodzi ndi bambo ndi mayi ake. Atafika mʼminda ya mpesa ya ku Timuna, anakumana ndi mkango ndipo unayamba kubangula. 6 Ndiyeno mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu,+ moti anakhadzula mkangowo pakati ngati mmene munthu angakhadzulire kamwana ka mbuzi ndi manja. Koma sanauze bambo kapena mayi ake zimene anachitazi. 7 Samisoni anapita kwa mkazi uja nʼkulankhula naye ndipo ankaonabe kuti mkaziyo anali woyenera.+
8 Patapita nthawi, Samisoni anabwerera kwa mkaziyo kuti akamʼtenge kupita naye kwawo.+ Ali mʼnjira, anapatuka kuti aone mkango umene anapha uja. Atafika anapeza kuti mkati mwa mkango wakufawo muli njuchi ndi uchi. 9 Ndiyeno anatengako uchiwo mʼmanja nʼkumadya akuyenda. Atapezananso ndi bambo ndi mayi ake, anawagawira uchiwo kuti nawonso adye. Koma sanawauze kuti uchiwo wautenga mkati mwa mkango wakufa.
10 Bambo ake anapita kwa mkazi uja, ndipo Samisoni anakonza phwando kumeneko, popeza zimenezi ndi zimene achinyamata ankachita. 11 Anthu akumeneko atamuona, anamubweretsera anyamata 30 kuti azikhala naye ngati anzake a mkwati. 12 Kenako Samisoni anawauza kuti: “Ndikufuna ndikuuzeni mwambi. Mukandiuza tanthauzo lake mʼmasiku 7 a phwandoli, ndidzakupatsani malaya 30 ndi zovala zina 30. 13 Koma mukalephera kundiuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa malaya 30 ndi zovala zina 30.” Atatero iwo anamuuza kuti: “Nena mwambi wakowo timve.” 14 Choncho iye anati:
“Mʼchinthu chodya zinzake munapezeka chakudya,
Ndipo mʼchinthu champhamvu munapezeka zotsekemera.”+
Iwo analephera kumasulira mwambiwo kwa masiku atatu. 15 Pa tsiku la 4 anauza mkazi wa Samisoni kuti: “Umunyengerere mwamuna wako+ kuti atiuze tanthauzo la mwambiwu. Akapanda kutiuza, tikuwotcha ndi moto pamodzi ndi nyumba ya bambo ako. Kodi mwatiitana kuti mudzatilande katundu wathu?” 16 Choncho mkazi wa Samisoni anayamba kulirira mwamuna wake, ndipo ankamuuza kuti: “Iwe umadana nane, sumandikonda.+ Wauza anthu a mtundu wanga mwambi, koma ine sunandiuze tanthauzo lake.” Atatero anamuuza kuti: “Ngakhale bambo kapena mayi anga sindinawauze. Ndiye iweyo ndikuuze chifukwa chiyani?” 17 Koma mkaziyo anapitiriza kulirira Samisoni mpaka pa tsiku la 7 la phwandolo. Pamapeto pake, pa tsiku la 7, Samisoni anauza mkaziyo tanthauzo lake chifukwa anamuumiriza. Kenako mkaziyo anauuza anthu a mtundu wake tanthauzo la mwambiwo.+ 18 Choncho pa tsiku la 7, dzuwa lisanalowe,* amuna amumzindawo anamuuza kuti:
“Kodi chotsekemera kuposa uchi nʼchiyani,
Nanga champhamvu kuposa mkango nʼchiyani?”+
Iye anawayankha kuti:
“Mukanapanda kulima ndi ngʼombe yanga yaikazi,+
Simukanatha kumasulira mwambi wanga.”
19 Ndiyeno mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu.+ Choncho anapita ku Asikeloni+ nʼkukapha amuna 30 akumeneko, ndipo anatenga zovala zawo nʼkuzipereka kwa anthu amene anamasulira mwambi aja.+ Iye anali wokwiya kwambiri pamene ankabwerera kunyumba ya bambo ake.
20 Kenako mkazi wa Samisoni+ anaperekedwa kuti akwatiwe ndi mmodzi mwa anyamata amene ankakhala ndi Samisoni ngati anzake a mkwati.+