1 Samueli
11 Ndiyeno Nahasi Muamoni+ anapita kukamanga msasa kuti amenyane ndi mzinda wa Yabesi+ ku Giliyadi. Zitatero, amuna onse a ku Yabesi anauza Nahasi kuti: “Tiyeni tichite pangano* ndipo tizikutumikirani.” 2 Nahasi Muamoni ananena kuti: “Ndichita nanu pangano pokhapokha ngati aliyense wa inu nditamuboola diso lake lakumanja. Ndichita zimenezi kuti ndichititse manyazi Aisiraeli onse.” 3 Akulu a ku Yabesi anayankha kuti: “Mutipatse masiku 7 kuti titumize uthenga mʼdziko lonse la Isiraeli, ngati sipapezeka wotipulumutsa, tidzadzipereka kwa inu.” 4 Kenako uthengawo unafika ku Gibeya,+ kwawo kwa Sauli ndipo anthu ataumva, onse anayamba kulira mokweza.
5 Ndiyeno Sauli anatulukira kuchokera kubusa akukusa ziweto ndipo anafunsa kuti: “Kodi chachitika nʼchiyani? Anthuwa akulira chiyani?” Choncho anamufotokozera zimene anthu a ku Yabesi ananena. 6 Sauli atamva zimenezo, mzimu wa Mulungu unamʼpatsa mphamvu+ ndipo anapsa mtima kwambiri. 7 Iye anatenga ngʼombe ziwiri zamphongo nʼkuzidula mapisi. Kenako anatuma anthu kuti akapereke mapisiwo mʼmadera onse a Isiraeli ndipo anati: “Aliyense amene satsatira Sauli ndi Samueli, izi nʼzimene zichitikire ngʼombe zake.” Anthu anagwidwa ndi mantha ochokera kwa Yehova, moti onse anapita mogwirizana.* 8 Iye atawerenga anthuwo ku Bezeki anapeza kuti Aisiraeli analipo 300,000, ndipo Ayuda analipo 30,000. 9 Kenako iwo anauza anthu amene anabwera ndi uthenga aja kuti: “Anthu a ku Yabesi ku Giliyadi mukawauze kuti, ‘Mawa masana* mupulumutsidwa.’” Zitatero anthuwo anafika ku Yabesi nʼkuuza anthu akumeneko uthengawo ndipo iwo anasangalala kwambiri. 10 Choncho anthu a ku Yabesi anauza Nahasi kuti: “Mawa tibwera kudzadzipereka kwa inu, ndipo mudzatichite chilichonse chimene mungafune.”+
11 Tsiku lotsatira, Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Anthuwo analowa pakati pa msasawo pa ulonda wamʼmawa.* Atatero, anayamba kupha Aamoni+ mpaka masana. Amene anapulumuka anawabalalitsa moti sipanapezeke anthu awiri ali limodzi. 12 Kenako anthu anauza Samueli kuti: “Amene ankanena kuti, ‘Sauli sangakhale mfumu yathuʼ+ aja ali kuti? Abweretseni kuno tiwaphe.” 13 Koma Sauli ananena kuti: “Lero pasaphedwe munthu aliyense,+ chifukwa Yehova wapulumutsa Isiraeli.”
14 Kenako Samueli anauza anthuwo kuti: “Tiyeni tipite ku Giligala+ kuti tikachitenso mwambo wolonga mfumu.”+ 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo analonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Kenako anapereka kwa Yehova nsembe zamgwirizano+ ndipo Sauli ndi amuna onse a Isiraeli anasangalala kwambiri.+