Yona
3 Yehova analankhula ndi Yona kachiwiri kuti:+ 2 “Nyamuka, upite kumzinda waukulu wa Nineve,+ ndipo ukalalikire uthenga umene ndikuuze.”
3 Choncho Yona ananyamuka nʼkupita ku Nineve+ pomvera mawu a Yehova.+ Mzinda wa Nineve unali waukulu kwambiri* ndipo mtunda wake unali woyenda masiku atatu. 4 Kenako Yona analowa mumzindawo nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.”
5 Anthu a ku Nineve anakhulupirira Mulungu+ ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli. 6 Uthengawo utafika kwa mfumu ya Nineve, mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu nʼkuvula chovala chake chachifumu. Kenako inavala chiguduli nʼkukhala paphulusa. 7 Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamula anthu kuti alengeze mu Nineve kuti:
“Mfumu ndi akuluakulu ake alamula kuti: Munthu aliyense, ngʼombe, nkhosa komanso chiweto chilichonse zisadye chilichonse. Munthu aliyense kapena chiweto zisadye chakudya kapena kumwa madzi. 8 Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo aliyense asiye zinthu zoipa komanso zachiwawa zimene amachita. 9 Ndani angadziwe, mwina Mulungu woona asintha maganizo pa zimene amafuna kuchita ndipo abweza mkwiyo wake woyaka moto, moti satiwononga?”
10 Mulungu woona ataona zimene anachita, kuti anasiya kuchita zoipa,+ anasintha maganizo ake ndipo sanawabweretsere tsoka limene ananena kuti awabweretsera.+