Genesis
48 Patapita nthawi Yosefe anauzidwa kuti: “Bambo anutu afooka.” Ndiyeno Yosefe anatenga ana ake awiri, Manase ndi Efuraimu nʼkupita kwa bambo akewo.+ 2 Kenako Yakobo anauzidwa kuti: “Mwana wanu Yosefe wabwera.” Choncho Isiraeli anadzuka modzilimbitsa nʼkukhala tsonga pabedi. 3 Yakobo anauza Yosefe kuti:
“Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine ku Luzi mʼdziko la Kanani nʼkundidalitsa.+ 4 Iye anandiuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana, ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu yambiri ya anthu.+ Dziko ili ndidzalipereka kwa mbadwa* zako kuti lidzakhale dziko lawo mpaka kalekale.’+ 5 Kuyambira lero ana awiri amene unabereka ku Iguputo kuno ine ndisanabwere, akhala anga.+ Efuraimu ndi Manase akhala ana anga ngati mmene alili Rubeni ndi Simiyoni.+ 6 Koma ana amene udzabereke pambuyo pa anawa, amenewo adzakhala ako. Iwo adzalandira mbali ya malo amene abale awo adzalandire ngati cholowa.+ 7 Kunena za ine, pamene ndinkachokera ku Padani, mayi ako Rakele anandifera+ panjira mʼdziko la Kanani, patatsala mtunda ndithu kuti tifike ku Efurata.+ Zitatero, ndinawaika mʼmanda panjira yopita ku Efurata, kapena kuti Betelehemu.”+
8 Ndiyeno Isiraeli ataona ana a Yosefe, anafunsa kuti: “Kodi awa ndi ndani?” 9 Yosefe anayankha bambo akewo kuti: “Ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kunoko.”+ Ndiyeno bambo akewo anati: “Tawabweretse kuno chonde, ndiwadalitse.”+ 10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba, moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anakisa anawo nʼkuwakumbatira. 11 Ndiyeno Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Sindinkayembekezera kuti ndingadzaonenso nkhope yako,+ koma pano Mulungu wandilola kuti ndionenso ana ako.” 12 Atatero, Yosefe anachotsa anawo pamawondo a Isiraeli. Kenako, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi.
13 Ndiyeno Yosefe anatenga ana ake awiriwo. Efuraimu+ anamuika kudzanja lake lamanja, kumanzere kwa Isiraeli. Ndipo Manase+ anamuika kudzanja lake lamanzere, kudzanja lamanja la Isiraeli. Atatero, anawabweretsa pafupi ndi bambo ake. 14 Koma Isiraeli anatambasula dzanja lake lamanja nʼkuliika pamutu pa Efuraimu, ngakhale kuti ndi amene anali wamngʼono. Anatambasulanso dzanja lake lamanzere nʼkuliika pamutu pa Manase. Anasemphanitsa dala manja ake chifukwa Manase ndi amene anali mwana woyamba.+ 15 Kenako anadalitsa Yosefe kuti:+
“Mulungu woona amene makolo anga Abulahamu ndi Isaki anayenda pamaso pake,+
Mulungu woona amene wakhala mʼbusa wanga moyo wanga wonse mpaka lero,+
16 Mngelo amene wakhala akundiwombola ku masoka anga onse,+ adalitse anyamatawa.+
Anawa azidziwika ndi dzina langa komanso mayina a makolo anga, Abulahamu ndi Isaki,
Anawa adzachulukane nʼkukhala gulu la anthu ambiri padziko lapansi.”+
17 Yosefe ataona kuti bambo ake aika dzanja lawo lamanja pamutu pa Efuraimu, sizinamusangalatse. Choncho, anagwira dzanja la bambo ake kuti alichotse pamutu pa Efuraimu nʼkuliika pamutu pa Manase. 18 Yosefe anauza bambo ake kuti: “Ayi bambo, musatero ayi. Mwana woyamba+ ndi uyu. Ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” 19 Koma bambo akewo anapitiriza kukana nʼkunena kuti: “Ndikudziwa mwana wanga, ndikudziwa zimenezo. Uyunso adzakhala mtundu wa anthu, ndipo adzakhala wamkulu. Koma mngʼono wakeyu adzakhala wamkulu kuposa iyeyu,+ ndipo mbadwa zake zidzachuluka kwambiri nʼkupanga mitundu ya anthu.”+ 20 Iye anapitiriza kuwadalitsa pa tsikulo+ kuti:
“Aisiraeli akamadalitsana azidzatchula dzina lako kuti,
‘Mulungu akudalitse ngati mmene anadalitsira Efuraimu ndi Manase.’”
Choncho Isiraeli anapitiriza kuika Efuraimu patsogolo pa Manase.
21 Kenako Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Taona, inetu ndikufa.+ Koma Mulungu adzakhalabe nanu ndithu anthu inu, ndipo adzakubwezerani kudziko la makolo anu.+ 22 Koma ine ndikukuwonjezera gawo limodzi la dziko kuposa abale ako, limene ndinalanda Aamori ndi lupanga langa komanso uta wanga.”