Nyimbo ya Solomo
1 Nyimbo yoposa nyimbo zonse, nyimbo ya Solomo:+
3 Kununkhira kwa mafuta ako ndi kosangalatsa.+
Dzina lako lili ngati mafuta onunkhira amene athiridwa pamutu.+
Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda.
4 Nditenge, tiye tithawe.
Chifukwatu mfumu yandipititsa mʼzipinda zake zamkati.
Tiye tikondwere komanso kusangalalira limodzi.
Tiye titamande* chikondi chimene umandisonyeza kuposa kutamanda vinyo.
Mpake kuti atsikana amakukonda.
5 Inu ana aakazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda koma wokongola,
Ngati matenti a ku Kedara+ komanso nsalu za matenti+ a Solomo.
6 Musandiyangʼanitsitse chifukwa chakuti ndada,
Ndi dzuwatu landidetsali.
Ana aamuna a mayi anga anandikwiyira.
Choncho anandiika kuti ndiziyangʼanira minda ya mpesa
Moti sindinathe kusamalira munda wanga wa mpesa.
7 Tandiuze, iwe amene ndimakukonda kwambiri,
Ndiuze kumene umakadyetsera ziweto zako,+
Kumene umakagonetsa ziweto masana.
Kodi ndikhalirenji ngati mkazi amene wafunda nsalu kumutu*
Pakati pa magulu a ziweto za anzako?”
8 “Ngati iweyo sukudziwa, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse,
Tsatira mapazi a ziweto
Ndipo ukadyetse mbuzi zako zingʼonozingʼono pafupi ndi matenti a abusa.”
9 “Iwe wokondedwa wanga, kwa ine uli ngati hatchi yaikazi yapamagaleta a Farao.+
10 Masaya ako amaoneka bwino ukavala zodzikongoletsera,*
Ndipo khosi lako limaoneka bwino ukavala mikanda.
12 “Pamene mfumu yakhala patebulo lake lozungulira,
13 Wachikondi wanga ali ngati kathumba konunkhira ka mule* kwa ine.+
Iye amakhala pakati pa mabere anga usiku wonse.
15 “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga.
Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa.”+
16 “Iwenso ndiwe wooneka bwino,* wachikondi wanga komanso ndiwe wosangalatsa.+
Bedi lathu ndi lamasamba ofewa.