2 Mbiri
22 Kenako anthu a ku Yerusalemu anaveka ufumu Ahaziya mwana wake wamngʼono kwambiri kuti alowe mʼmalo mwake chifukwa gulu la achifwamba limene linabwera ndi Aluya kumsasa linapha ana ake onse akuluakulu.+ Choncho Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.+ 2 Ahaziya anakhala mfumu ali ndi zaka 22 ndipo analamulira ku Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake dzina lawo linali Ataliya+ mdzukulu* wa Omuri.+
3 Ahaziya nayenso anayenda mʼnjira za anthu a mʼbanja la Ahabu+ chifukwa amayi ake ndi amene anali mlangizi wake kuti azichita zoipa. 4 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira anthu a mʼbanja la Ahabu, chifukwa iwowo anakhala alangizi ake pambuyo pa imfa ya bambo ake ndipo anamʼpweteketsa. 5 Anatsatira malangizo awo ndipo anapita kunkhondo ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli, kukamenyana ndi Hazaeli+ mfumu ya Siriya ku Ramoti-giliyadi.+ Kumeneko oponya mivi anavulaza Yehoramu. 6 Choncho Yehoramu anabwerera nʼkupita ku Yezereeli+ kuti akachire mabala amene anamʼvulaza ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+
Ahaziya* mwana wa Yehoramu+ mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu+ mwana wa Ahabu chifukwa anali atavulazidwa.*+ 7 Koma Mulungu ndi amene anachititsa kuti Ahaziya apite kwa Yehoramu kuti akaphedwe. Atafika kumeneko, anatengana ndi Yehoramu nʼkupita kukakumana ndi Yehu+ mdzukulu* wa Nimusi, amene Yehova anamudzoza kuti aphe anthu a mʼbanja la Ahabu.+ 8 Yehu atayamba kupereka chiweruzo kwa anthu a mʼbanja la Ahabu, anapeza akalonga a Yuda ndi ana a abale ake a Ahaziya, omwe ankatumikira Ahaziya, ndipo anawapha.+ 9 Kenako iye anayamba kufunafuna Ahaziya ndipo anthu anakamugwira ku Samariya kumene ankabisala nʼkupita naye kwa Yehu. Atatero iwo anamupha nʼkumuika mʼmanda+ popeza anati: “Uyu ndi mdzukulu wa Yehosafati yemwe anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”+ Panalibe aliyense wa mʼbanja la Ahaziya amene akanatha kukhala mfumu ya ufumuwo.
10 Ataliya, mayi ake a Ahaziya+ ataona kuti mwana wake wafa, anapha anthu onse amene anali oyenera kulowa ufumu* wa Yuda.+ 11 Koma Yehosabati mwana wamkazi wa mfumu, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pagulu la ana aamuna a mfumu amene ankayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi ndi mayi amene ankamusamalira nʼkukamubisa mʼchipinda chamkati chogona. Yehosabati, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu,+ (ameneyu anali mkazi wa wansembe Yehoyada+ komanso mchemwali wake wa Ahaziya) anakwanitsa kubisa mwanayo kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe.+ 12 Anakhala naye kwa zaka 6, atamubisa mʼnyumba ya Mulungu woona pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.