1 Samueli
22 Choncho Davide anachoka kumeneko+ nʼkuthawira kuphanga la Adulamu.+ Azichimwene ake ndi anthu onse amʼnyumba ya bambo ake atamva zimenezi, ananyamuka nʼkumutsatira. 2 Anthu onse amene anali pa mavuto, onse amene anali ndi ngongole, ndi onse amene anali ndi madandaulo anasonkhana kwa iye, ndipo iye anakhala mtsogoleri wawo. Amuna onse amene anali naye analipo 400.
3 Kenako Davide anapita ku Mizipe, ku Mowabu ndipo anauza mfumu ya Mowabu+ kuti: “Ndikupempha kuti bambo ndi mayi anga azikhala nawo kuno mpaka nditadziwa zimene Mulungu andichitire.” 4 Choncho anawasiya kuti azikhala ndi mfumu ya Mowabu, moti iwo anakhala kumeneko nthawi yonse imene Davide ankabisala kumalo ovuta kufikako.+
5 Patapita nthawi, Gadi,+ yemwe anali mneneri, anauza Davide kuti: “Usakhalenso kumalo ovuta kufikako. Chokako kumeneko ndipo upite mʼdziko la Yuda.”+ Choncho Davide anachoka nʼkupita kunkhalango ya Hereti.
6 Sauli anamva kuti Davide ndi anthu amene anali naye apezeka. Pa nthawiyi Sauli anali ku Gibeya+ atakhala pansi pa mtengo wa bwemba, pamalo okwezeka. Iye anali ndi mkondo mʼmanja ndipo atumiki ake onse anali atamuzungulira. 7 Kenako Sauli anauza atumiki akewo kuti: “Tamverani inu a fuko la Benjamini. Kodi mwana wa Jese+ nayenso adzakupatsani nonsenu minda ya mpesa ndi minda ya mbewu zina? Kodi nonsenu adzakuikani kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000 ndi atsogoleri a magulu a anthu 100?+ 8 Nonsenu mwandikonzera chiwembu. Pamene mwana wanga anachita pangano ndi mwana wa Jese,+ palibe amene anandiuza. Palibenso amene wandichitira chifundo nʼkundiuza kuti mwana wanga weniweni wachititsa mtumiki wanga kundibisalira ngati mmene zililimu.”
9 Kenako Doegi+ wa ku Edomu, mkulu wa atumiki a Sauli anayankha kuti:+ “Ineyo ndinaona mwana wa Jese atabwera ku Nobu kwa Ahimeleki, mwana wa Ahitubu.+ 10 Ahimeleki anafunsira kwa Yehova mʼmalo mwa Davide ndipo anamʼpatsa chakudya. Mpaka anamupatsanso lupanga la Goliyati Mfilisiti.”+ 11 Nthawi yomweyo mfumu inatumiza anthu kuti akaitane Ahimeleki wansembe, mwana wa Ahitubu komanso ansembe onse amʼnyumba ya bambo ake omwe anali ku Nobu. Choncho onse anabwera kwa mfumu.
12 Ndiyeno Sauli anati: “Tamvera iwe mwana wa Ahitubu.” Ahimeleki anayankha kuti: “Ndikumva mbuyanga.” 13 Sauli anapitiriza kumuuza kuti: “Nʼchifukwa chiyani iweyo ndi mwana wa Jese mwandikonzera chiwembu? Iweyo unamʼpatsa mkate ndi lupanga komanso unamufunsira kwa Mulungu. Iye wandiukira ndipo panopa wandibisalira.” 14 Ahimeleki anayankha mfumuyo kuti: “Pa atumiki anu onse ndi ndani ali wokhulupirika* ngati Davide?+ Iye ndi mkamwini wa mfumu,+ mtsogoleri wa asilikali okulonderani ndiponso munthu wolemekezeka mʼnyumba yanu.+ 15 Kodi ndayamba lero kumufunsira kwa Mulungu?+ Sindingachite zimene mukunenazo! Chonde mfumu musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu ndiponso anthu onse amʼnyumba ya bambo anga, chifukwa ine mtumiki wanu sindinadziwe chilichonse pa nkhaniyi.”+
16 Koma mfumu inati: “Ufa ndithu+ Ahimeleki, iweyo ndi anthu onse amʼnyumba ya bambo ako.”+ 17 Kenako Sauli anauza asilikali othamanga amene anali atamuzungulira kuti: “Iphani ansembe a Yehova chifukwa ali kumbali ya Davide! Iwo ankadziwa kuti Davide akuthawa, koma sanandiuze!” Komabe atumiki a mfumuwo sanafune kupha ansembe a Yehova. 18 Ndiyeno mfumu inauza Doegi+ kuti: “Iwe, ipha ansembewa!” Nthawi yomweyo Doegi wa ku Edomu+ anapha ansembewo. Tsiku limenelo anapha amuna 85 ovala efodi wa nsalu.+ 19 Iye anaphanso anthu amumzinda wa Nobu+ womwe unali mzinda wa ansembe. Anapha amuna ndi akazi, ana ndi ana oyamwa omwe, ngʼombe ndi abulu komanso nkhosa.
20 Koma mwana mmodzi wamwamuna wa Ahimeleki, mwana wa Ahitubu, dzina lake Abiyatara+ anapulumuka ndipo anathawa nʼkutsatira Davide. 21 Abiyatara anauza Davide kuti: “Sauli wapha ansembe a Yehova.” 22 Ndiyeno Davide anauza Abiyatara kuti: “Tsiku lomwe lija+ nditangoona kuti Doegi wa ku Edomu aliko, ndinadziwa kuti akauza Sauli. Ineyo ndi amene ndachititsa kuti anthu onse amʼnyumba ya bambo ako aphedwe. 23 Koma iwe khala ndi ine ndipo usachite mantha. Chifukwa aliyense amene akufunafuna moyo wako akufunafunanso moyo wanga, ndipo ndikuteteza.”+