1 Samueli
27 Koma Davide anaganiza kuti: “Tsiku lina Sauli adzandipha ndithu. Chanzeru chimene ndingachite nʼkuthawira+ kudziko la Afilisiti. Ndiyeno Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Isiraeli+ ndipo ndidzapulumuka mʼmanja mwake.” 2 Choncho Davide pamodzi ndi amuna 600+ amene ankayenda naye anapita kwa Akisi+ mfumu ya ku Gati, mwana wa Maoki. 3 Davide ankakhala ndi Akisi ku Gati pamodzi ndi amuna amene ankayenda naye, ndipo aliyense anali ndi banja lake. Davide anali ndi akazi awiri, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala. 4 Sauli atamva kuti Davide wathawira ku Gati, anasiya kumusakasaka.+
5 Kenako Davide anauza Akisi kuti: “Ngati mungandikomere mtima, ndimapempha kuti andipatseko malo mumzinda umodzi wakutali kuti ndikakhale kumeneko. Palibe chifukwa choti ine mtumiki wanu ndizikhala limodzi ndi inu mumzinda wachifumu.” 6 Choncho pa tsikuli Akisi anapatsa Davide mzinda wa Zikilaga.+ Nʼchifukwa chake mzinda wa Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda mpaka lero.
7 Nthawi* yonse imene Davide anakhala mumzinda wakutali wa Afilisiti inali chaka chimodzi ndi miyezi 4.+ 8 Davide ndi amuna amene ankayenda naye ankapita kukamenyana ndi Agesuri,+ Agirezi ndi Aamaleki.+ Anthu amenewa ankakhala mʼdera loyambira ku Telami kukafika ku Shura,+ mpaka kudziko la Iguputo. 9 Davide akapita kunkhondo sankasiya mwamuna kapena mkazi aliyense wamoyo.+ Iye ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamila ndi zovala ndipo akatero ankabwerera kwa Akisi. 10 Akisi akafunsa kuti: “Kodi lero munakamenya kuti nkhondo?” Davide ankayankha kuti: “Kumʼmwera kwa dziko* la Yuda”+ kapena “Kumʼmwera kwa dziko la Ayerameeli”+ kapena “Kumʼmwera kwa dziko la Akeni.”+ 11 Davide sankasiya mwamuna kapena mkazi aliyense wamoyo nʼkubwerera naye ku Gati, chifukwa ankaganiza kuti: “Angayambe kukatinenera kuti, ‘Davide wachita zakutizakuti.’” (Izi nʼzimene iye ankachita pa nthawi yonse imene anakhala mumzinda wakutali wa Afilisiti.) 12 Akisi ankamukhulupirira Davide, ndipo mumtima mwake ankati: ‘Ndithu, Davide wakhala ngati fungo lonunkha kwa Aisiraeli anzake, ndipo adzakhalabe mtumiki wanga.’