Numeri
5 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti azitulutsa mumsasa munthu aliyense wakhate,+ aliyense wakukha kumaliseche+ komanso aliyense wodetsedwa chifukwa chokhudza munthu wakufa.+ 3 Kaya akhale mwamuna kapena mkazi, uziwatulutsa mumsasa kuti asadetse+ misasa ya anthu amene ine ndikukhala pakati pawo.”+ 4 Choncho Aisiraeli anachitadi zomwezo moti anatulutsa anthuwo kunja kwa msasa, mogwirizana ndi zimene Yehova anauza Mose.
5 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 6 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi wachita machimo alionse amene anthu amachita, nʼkuchita zinthu mosakhulupirika pamaso pa Yehova, munthu ameneyo wapalamula mlandu.+ 7 Munthuyo aziulula+ tchimo limene wachita. Azipereka malipiro onse a mlandu wake, komanso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a malipirowo.+ Azipereka malipirowo kwa munthu amene wamulakwira. 8 Koma ngati munthu amene walakwiridwayo wamwalira ndipo alibe wachibale wapafupi amene angalandire malipiro a mlanduwo, malipirowo aziperekedwa kwa Yehova kuti akhale a wansembe. Munthu amene wachimwayo aziperekanso nkhosa yamphongo yoti wansembeyo amuphimbire machimo ake.+
9 Zopereka zonse za zinthu zopatulika,+ zimene Aisiraeli azipereka kwa wansembe, zizikhala zake.+ 10 Zinthu zopatulika za munthu aliyense zizikhala zake. Chilichonse chimene munthu angapereke kwa wansembe, chizikhala cha wansembeyo.’”
11 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12 “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Muzichita izi ngati mkazi wazembera mwamuna wake nʼkuchita zosakhulupirika 13 mwakuti mwamuna wina wagona naye,+ koma mwamuna wake sanadziwe komanso palibe aliyense amene wadziwa. Muzichita zimenezi ngati mkaziyo wadzidetsa, koma palibe munthu amene angachitire umboni za nkhaniyo komanso sanagwidwe: 14 Ngati mwamuna wake akuchita nsanje ndipo akukayikira kuti mkazi wake wachita chigololo nʼkudzidetsa pamene mkaziyo wachitadi chigololo, kapena ngati akuchita nsanje nʼkumakayikira kuti mkazi wake wachita chigololo pamene mkaziyo sanachite, 15 mwamunayo azitenga mkaziyo nʼkupita naye kwa wansembe. Azipita ndi nsembe ya mkaziyo ya ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo asamauthire mafuta kapena lubani chifukwa ndi nsembe yambewu yansanje, nsembe yambewu yokumbutsa cholakwa.
16 Wansembeyo azitenga mkaziyo nʼkumuimiritsa pamaso pa Yehova.+ 17 Kenako azitenga madzi opatulika mʼchiwiya chadothi. Azitengakonso fumbi lapansi mʼchihema, nʼkulithira mʼmadziwo. 18 Ndiyeno wansembeyo aziimiritsa mkaziyo pamaso pa Yehova nʼkumumasula chovala cha kumutu kwake. Kenako, azitenga nsembe yambewu yachikumbutso, yomwe ndi nsembe yambewu yansanje,+ nʼkuiika mʼmanja mwa mkaziyo. Wansembeyo azitenga mʼdzanja lake madzi owawa obweretsa temberero.+
19 Wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo pomuuza kuti: “Ngati mwamuna aliyense sanagone nawe ndipo ngati sunamʼzembere mwamuna wako pamene uli mʼmanja mwake+ nʼkuchita chodetsa chilichonse, madzi owawa obweretsa tembererowa asakuvulaze. 20 Koma ngati unazembera mwamuna wako pamene uli mʼmanja mwake nʼkudzidetsa, moti wagona ndi mwamuna wina—”*+ 21 Wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo ndi lumbiro limene likuphatikizapo temberero. Iye aziuza mkaziyo kuti: “Yehova akuike kukhala chitsanzo cha temberero ndi lumbiroli pakati pa anthu a mtundu wako. Yehova achite zimenezo pofotetsa* ntchafu* yako ndi kutupitsa mimba yako. 22 Madzi a tembererowa alowe mʼmatumbo mwako kuti akatupitse mimba yako ndi kufotetsa* ntchafu* yako.” Ndipo mkaziyo aziyankha kuti: “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”*
23 Kenako wansembeyo azilemba matemberero amenewa mʼbuku ndipo aziwafufuta mʼmadzi owawa aja. 24 Akatero azimwetsa mkaziyo madzi owawa a tembererowo, ndipo madziwo akalowa mʼthupi mwake, mkaziyo azimva ululu. 25 Ndiyeno wansembeyo azitenga nsembe yambewu yansanje+ imene ili mʼmanja mwa mkaziyo, nʼkuiyendetsa uku ndi uku pamaso pa Yehova. Akatero, aziibweretsa pafupi ndi guwa lansembe. 26 Wansembeyo azitapako nsembe yambewuyo kuimira nsembe yonseyo, nʼkuiwotcha paguwa lansembe.+ Pambuyo pake, azipatsa mkaziyo madziwo kuti amwe. 27 Akamumwetsa madziwo, ngati iye anadzidetsa pogona ndi mwamuna wina, madzi a tembererowo azikhala chinthu chowawa akalowa mʼthupi mwake. Zikatero mimba yake izitupa ndipo ntchafu* yake izifota.* Mkaziyo azikhala chitsanzo cha munthu wotembereredwa pakati pa anthu a mtundu wake. 28 Koma ngati mkaziyo ali woyera chifukwa sanadzidetse, chilangocho chisamamugwere, ndipo azitha kukhala woyembekezera nʼkubereka ana.
29 Limeneli ndi lamulo pa nkhani ya nsanje,+ pamene mkazi wazembera mwamuna wake, nʼkudzidetsa ali mʼmanja mwa mwamuna wakeyo, 30 kapena ngati mwamuna akuchita nsanje ndipo akuganiza kuti mkazi wake sanayende bwino. Zikatero, mwamunayo azibwera ndi mkazi wake pamaso pa Yehova, ndipo wansembe azichita zonse zofunika pa mkaziyo mogwirizana ndi lamulo limeneli. 31 Mwamunayo adzakhala wopanda mlandu, koma mkazi wake adzalandira chilango chifukwa cha kulakwa kwake.’”