Miyambo
24 Usamasirire anthu oipa,
Ndipo usamalakelake utakhala pagulu lawo,+
2 Chifukwa mtima wawo umangoganizira zochita chiwawa,
Ndipo milomo yawo imangokhalira kulankhula zobweretsera ena mavuto.
4 Kudziwa zinthu kumachititsa kuti zipinda za nyumbayo zidzaze
Ndi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.+
7 Kwa munthu wopusa nʼzosatheka kupeza nzeru zenizeni.+
Ndipo amakhala alibe chilichonse choti anganene pageti la mzinda.
9 Mapulani a munthu* wopusa amamupangitsa kuti achite tchimo,
Ndipo anthu amanyansidwa ndi munthu wonyoza.+
10 Ukafooka pa nthawi imene ukukumana ndi mavuto,
Mphamvu zako zidzachepa.
11 Pulumutsa anthu amene atengedwa kuti akaphedwe,
Ndipo amene akuyenda modzandira popita kukaphedwa uwathandize.+
12 Ukanena kuti: “Ifetu zimenezi sitimazidziwa,”
Kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimene zili mʼmaganizo mwako?+
Ndithudi, amene amakuyangʼanitsitsa adzadziwa
Ndipo adzabwezera munthu aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+
13 Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino.
Uchi wochokera pazisa za njuchi umatsekemera.
14 Mofanana ndi zimenezi, dziwa kuti nzeru ndi zabwino kwa iwe.*+
Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino
Ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+
15 Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pafupi ndi nyumba yake kuti umuchitire chiwembu.
Usamawononge malo ake okhala.
16 Chifukwa munthu wolungama akhoza kugwa maulendo 7 ndipo adzadzukanso,+
Koma anthu oipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzagwa.+
17 Mdani wako akagwa usamasangalale,
Ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere.+
18 Ukachita zimenezi Yehova adzaona ndipo zidzamuipira
Moti adzachotsa mkwiyo wake pa mdani wakoyo.+
19 Usamapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa.
Usamasirire anthu oipa,
20 Chifukwa aliyense woipa alibe tsogolo,+
Ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+
21 Mwana wanga uziopa Yehova komanso mfumu.+
Ndipo usamakhale pagulu la anthu ofuna kuti zinthu zisinthe,+
Ndipo ndi ndani amene angadziwe za tsoka limene onsewa* adzawabweretsere?+
23 Mawu awanso ndi a anthu anzeru:
Si bwino kukondera poweruza mlandu.+
24 Aliyense amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wolungama,”+
Anthu adzamutemberera ndipo mitundu ya anthu idzaitanira tsoka pa iye.
25 Koma anthu amene amamudzudzula zinthu zidzawayendera bwino.+
Adzalandira madalitso a zinthu zabwino.+
26 Anthu adzakisa milomo ya munthu amene amayankha moona mtima.*+
27 Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo uonetsetse kuti ntchito yonse yatheka mʼmunda wako.
Ukatero ukamange nyumba yako.*
28 Usapereke umboni wotsutsana ndi mnzako ngati ulibe umboni weniweni.+
Usapusitse anthu ena ndi milomo yako.+
31 Ndinaona kuti munali tchire lokhalokha.
Zitsamba zoyabwa zinali paliponse mʼmundamo,
Komanso mpanda wake wamiyala unali utagumuka.+
32 Nditaona zimenezi, ndinayamba kuziganizira mumtima mwanga,
Ndipo ndinaphunzirapo kuti: