2 Samueli
14 Yowabu, mwana wa Zeruya+ anadziwa kuti mfumu ikulakalaka Abisalomu.+ 2 Choncho Yowabu anatumiza anthu ku Tekowa+ kuti akatenge mayi wochenjera. Atabwera naye, anamuuza kuti: “Chonde ukhale ngati munthu amene akulira maliro, uvale zovala zolirira maliro komanso usadzole mafuta.+ Ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira maliro kwa nthawi yaitali. 3 Ndiyeno upite kwa amfumu ndipo ukawauze mawu awa.” Atatero, Yowabu anamuuza zokanena.*
4 Mayi wa ku Tekowayo anapita kukaonana ndi mfumu, ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi, kenako anadzigwetsa, nʼkunena kuti: “Chonde mfumu ndithandizeni!” 5 Ndiyeno mfumu inamufunsa kuti: “Chavuta nʼchiyani?” Mayiyo anayankha kuti: “Ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira. 6 Ine mtumiki wanu ndinali ndi ana awiri aamuna. Tsiku lina anawo ali kutchire anayamba kumenyana ndipo panalibe wowaleretsa. Ndiyeno wina anapha mnzake. 7 Panopa banja lonse landiukira ine mtumiki wanu ndipo aliyense akunena kuti, ‘Bweretsa wopha mchimwene wakeyo kuti timuphe chifukwa cha mchimwene wake amene anamupha.+ Kaya zimenezi zipangitsa kuti pasakhale wolandira cholowa, palibe vuto.’ Anthuwa adzazimitsa khala limene latsala ndipo adzasiya mwamuna wanga wopanda dzina komanso mbewu yotsala padziko lapansi.”
8 Ndiyeno mfumu inauza mayiyo kuti: “Pita kunyumba kwanu ndipo ine ndipereka lamulo lokhudza nkhani imeneyi.” 9 Mayi wa ku Tekowayo anauza mfumu kuti: “Mbuyanga mfumu, wolakwa ndikhale ine ndi anthu amʼnyumba ya bambo anga, koma inu mfumu, ndi mpando wanu wachifumu, ndinu osalakwa.” 10 Kenako mfumu inanena kuti: “Ngati aliyense angalankhule nawenso za nkhani imeneyi, ubwere naye kwa ine ndipo sadzakuvutitsanso.” 11 Koma mayiyo anati: “Chonde mfumu, kumbukirani Yehova Mulungu wanu kuti munthu wobwezera magazi+ asachite zoipa zina komanso asaphe mwana wanga.” Ndiyeno mfumu inati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo,+ ngakhale tsitsi limodzi la mwana wako siligwa pansi.” 12 Ndiyeno mkaziyo anati: “Mbuyanga mfumu, chonde ndiloleni ine mtumiki wanu kuti ndikuuzeni mawu amodzi.” Mfumu inamuuza kuti: “Lankhula!”
13 Mayiyo ananena kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu mfumu mwachitira anthu a Mulungu zinthu ngati zimenezi?+ Zimene inu mfumu mwalankhulazi, zikusonyeza kuti ndinu wolakwa chifukwa munathamangitsa mwana wanu ndipo simunamuitanitse kuti abwerenso.+ 14 Tonsefe tidzafa ndipo tidzakhala ngati madzi otayika amene sawoleka. Koma Mulungu satenga moyo ndipo amaganizira zifukwa zoti munthu amene wathamangitsidwa asakhalebe wothamangitsidwa. 15 Ndabwera kudzakuuzani zimenezi mbuyanga mfumu chifukwa anthu andichititsa mantha. Moti ine mtumiki wanu ndinati, ‘Bwanji ndikalankhule ndi mfumu. Mwina mfumu idzamvera zimene kapolo wake wapempha. 16 Mfumu ikhoza kundimvera nʼkundipulumutsa kwa munthu amene akufuna kupha ineyo komanso mwana wanga mmodzi yekhayo kuti tisalandire cholowa chomwe Mulungu anatipatsa.’+ 17 Ndiye ine mtumiki wanu ndinati, ‘Mawu a mbuyanga mfumu anditonthoze,’ popeza inu mbuyanga muli ngati mngelo wa Mulungu woona, posiyanitsa chabwino ndi choipa. Yehova Mulungu wanu akhale nanu.”
18 Ndiyeno mfumu inauza mayiyo kuti: “Usandibisire chilichonse pa zimene ndikufuna kukufunsa.” Mayiyo ananena kuti: “Lankhulani mbuyanga mfumu.” 19 Kenako mfumu inamufunsa kuti: “Kodi Yowabu ndi amene wakutuma?”+ Mayiyo anayankha kuti: “Ndikulumbira pali moyo wanu mbuyanga mfumu, zimene inu mwanena mbuyanga nʼzoona. Mtumiki wanu Yowabu ndi amene wandituma kuti ndidzanene zonse zomwe ndalankhulazi. 20 Mtumiki wanu Yowabu wachita zimenezi kuti musinthe mmene mukuonera nkhaniyi. Koma inu mbuyanga muli ndi nzeru ngati mngelo wa Mulungu woona, moti mukudziwa zonse zimene zikuchitika mʼdzikoli.”
21 Zitatero, mfumu inauza Yowabu kuti: “Chabwino, ndichita zimene wanena.+ Pita ukatenge mnyamatayo Abisalomu ndipo ubwere naye.”+ 22 Yowabu atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi ndipo anatamanda mfumu. Yowabu anati: “Ine mtumiki wanu ndadziwa kuti lero mwandikomera mtima, mbuyanga mfumu, chifukwa inu mfumu mwamvera zimene ine mtumiki wanu ndapempha.” 23 Kenako Yowabu anapita ku Gesuri+ ndipo anakatenga Abisalomu nʼkubwera naye ku Yerusalemu. 24 Koma mfumu inanena kuti: “Apite kunyumba kwake, asaonane nane.” Choncho Abisalomu anapita kunyumba kwake, ndipo sanaonane ndi mfumu.
25 Mu Isiraeli munalibe mwamuna amene anthu ankamuona kuti ndi wooneka bwino kwambiri koposa Abisalomu. Iye analibe chilema chilichonse kuyambira kuphazi mpaka pamutu. 26 Abisalomu ankameta tsitsi lake kumapeto kwa chaka chilichonse chifukwa linkamulemera kwambiri. Ndipo akameta tsitsi lakelo, linkalemera masekeli 200* akaliyeza ndi mwala wachifumu woyezera kulemera kwa zinthu.* 27 Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu+ ndi wamkazi mmodzi, dzina lake Tamara. Iye anali mtsikana wokongola kwambiri.
28 Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu koma sanaonane ndi mfumu.+ 29 Kenako, Abisalomu anaitanitsa Yowabu kuti amutume kwa mfumu, koma Yowabu sanapite kwa Abisalomu. Iye anamuitanitsanso kachiwiri, koma anakana. 30 Zitatero, Abisalomu anauza atumiki ake kuti: “Pafupi ndi munda wanga pali munda wa Yowabu ndipo muli balere. Mupite mukautenthe.” Choncho atumiki a Abisalomu anapita nʼkukawotchadi mundawo. 31 Ndiyeno Yowabu anapita kunyumba kwa Abisalomu kukamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani atumiki ako awotcha munda wanga?” 32 Abisalomu anayankha kuti: “Ine ndinakutumizira uthenga wakuti, ‘Ubwere kuno ndikutume kwa mfumu ukanene kuti: “Nʼchifukwa chiyani ndinabwerako ku Gesuri?+ Zikanakhala bwino ndikanangokhala komweko. Ndikufuna ndionane ndi mfumu, ndipo ngati ndili wolakwa, mfumu indiphe.”’”
33 Choncho Yowabu anapita kwa mfumu nʼkukanena mawu amenewa. Ndiyeno mfumu inaitanitsa Abisalomu ndipo iye anapita. Atafika anagwada nʼkuwerama, kenako anadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Zitatero, mfumu inamukisa Abisalomu.+