Hoseya
Koma anapezeka ndi mlandu wolambira Baala+ ndipo anafa.
2 Tsopano iwo akuchita machimo ena,
Ndipo akugwiritsa ntchito siliva wawo popanga zifaniziro zachitsulo.+
Amapanga mafano mwaluso, koma zonsezi ndi ntchito za amisiri.
Iwo amauza mafanowo kuti, ‘Amuna opereka nsembe akise mafano a ana angʼombe.’+
3 Choncho iwo adzakhala ngati mitambo ya mʼmawa,
Ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma.
Adzakhalanso ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo kuchokera pamalo opunthira mbewu,
Ndiponso ngati utsi umene umatuluka mʼchumuni kudenga.
4 Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+
Palibe Mulungu wina amene unkamudziwa kupatula ine.
Palibenso mpulumutsi wina kupatula ine.+
5 Ine ndinakudziwa uli mʼchipululu,+ mʼdziko la chilala.
Choncho unandiiwala.+
8 Ndidzawaukira ngati chimbalangondo chimene ana ake asowa,
Ndipo ndidzawangʼamba pachifuwa,
Kumeneko ndidzawadya ngati mkango.
Chilombo chakutchire chidzawakhadzulakhadzula.
9 Chidzakuwononga iwe Isiraeli
Chifukwa chakuti unandisiya ine mthandizi wako.
10 Ndiye ili kuti mfumu yako, kuti ikupulumutse mʼmizinda yako yonse?+
Olamulira* ako ali kuti amene unawauza kuti,
‘Ndipatseni mfumu ndiponso akalongaʼ?+
13 Zowawa ngati za mkazi amene akubereka zidzamugwera.
Koma iye ndi mwana wopanda nzeru,
Chifukwa nthawi yoti abadwe ikakwana, sadzabwera kuti atuluke.
Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+
Iwe Manda, kodi mphamvu yako yowononga ili kuti?+
Koma Efuraimu sindimumvera chisoni.
15 Ngakhale atakula bwino pakati pa bango,
Mphepo yakumʼmawa idzabwera, mphepo ya Yehova.
Idzabwera kuchokera kuchipululu nʼkuumitsa chitsime chake ndi kasupe wake.
Winawake adzawononga chuma chake chonse chamtengo wapatali.+
16 Samariya adzaimbidwa mlandu+ chifukwa wagalukira Mulungu wake.+
Iwo adzagwetsedwa ndi lupanga.+
Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa.
Ndipo akazi awo apakati adzatumbulidwa.”