Yesaya
20 Mʼchaka chimene Tatani* anatumizidwa ku Asidodi+ ndi Mfumu Sarigoni ya Asuri, anamenyana ndi mzindawo nʼkuulanda.+ 2 Pa nthawi imeneyo Yehova analankhula kudzera mwa Yesaya+ mwana wa Amozi kuti: “Pita ukavule chiguduli chimene chili mʼchiuno mwako komanso nsapato zimene zili kuphazi kwako.” Iye anachitadi zimenezo, nʼkumayenda ali maliseche* ndiponso wopanda nsapato.
3 Kenako Yehova anati: “Mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu, kuti akhale chizindikiro+ ndi chenjezo kwa Iguputo+ ndi Itiyopiya.+ 4 Mofanana ndi zimenezi, mfumu ya Asuri idzagwira gulu la anthu ku Iguputo+ ndi ku Itiyopiya nʼkupita nawo ku ukapolo kudziko lina. Idzagwira anyamata ndi amuna achikulire, ali opanda zovala ndi opanda nsapato, ndiponso matako awo ali pamtunda moti Iguputo adzachititsidwa manyazi. 5 Iwo adzachita mantha komanso adzachita manyazi ndi Itiyopiya amene ankamudalira ndiponso ndi Iguputo amene ankamunyadira.* 6 Pa tsiku limenelo, anthu okhala mʼdziko limeneli lamʼmphepete mwa nyanja adzanena kuti, ‘Taonani zimene zachitikira dziko limene tinkalidalira lija, kumene tinathawirako kuti litithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya Asuri! Ndiye atipulumutse ndi ndani tsopano?’”