Amosi
4 “Tamverani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basana,
Amene mumakhala mʼphiri la Samariya,+
Inu akazi amene mukuchitira zachinyengo anthu ovutika+ komanso kuphwanya anthu osauka.
Ndipo mumauza amuna* anu kuti, ‘Tipatseni chakumwa kuti timwe!’
2 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walumbira mogwirizana ndi kuyera kwake kuti,
‘“Taonani! Masiku adzafika pamene iye adzakukolani ndi ngowe zokolera nyama nʼkukunyamulani.
Ndipo otsala adzawakola ndi mbedza.
3 Mudzatulukira pamabowo a mpanda amene muli nawo pafupi.
Ndipo mudzaponyedwa kunja, ku Harimoni,” watero Yehova.’
4 ‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa,*+
Bwerani ku Giligala kuti mudzawonjezere machimo.+
5 Perekani nsembe zoyamikira za mkate wokhala ndi zofufumitsa.+
Ndipo lengezani mokweza za nsembe zanu zaufulu!
Chifukwa nʼzimene mumakonda kuchita, inu Aisiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
6 ‘Mʼmizinda yanu yonse, ine sindinakupatseni chakudya.
Ndipo ndinachititsa kuti mʼnyumba zanu zonse musakhale chakudya.+
Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.
7 ‘Ine ndinakumanani mvula kutatsala miyezi itatu kuti mukolole.+
Ndinagwetsa mvula mumzinda wina koma mumzinda wina sindinagwetse.
Mvula inagwa mʼmunda umodzi
Koma mʼmunda wina, mmene simunagwe mvula, munauma.
8 Anthu amʼmizinda iwiri kapena itatu anayenda movutikira kupita mumzinda wina kuti akamwe madzi,+
Ndipo ludzu lawo silinathe,
Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.
9 ‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso matenda a chuku.+
Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina.
Koma dzombe linawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+
Ndipo inu simunabwererebe kwa ine,’+ watero Yehova.
10 ‘Ndinakutumizirani mliri ngati wa ku Iguputo.+
Ndinapha anyamata anu ndi lupanga+ ndipo mahatchi anu analandidwa.+
Ndinachititsa kuti fungo lonunkha lamʼmisasa yanu lifike mʼmphuno mwanu,+
Koma inu simunabwerere kwa ine,’ watero Yehova.
Ndipo inu munali ngati chikuni cholanditsidwa pamoto.
Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.
12 Ndidzakuchitiranso zimenezo, iwe Isiraeli.
Ndipo chifukwa chakuti ndidzakuchitira zimenezi,
Konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Isiraeli.