Genesis
45 Zitatero Yosefe analephera kudzigwira pamaso pa atumiki ake onse.+ Ndiyeno anafuula kuti: “Aliyense atuluke muno!” Choncho panalibe aliyense amene anali naye pamene Yosefe ankadziulula kwa abale ake.+
2 Atatero, anayamba kulira mokweza mawu mpaka Aiguputo ndiponso anthu akunyumba ya Farao anamva. 3 Kenako Yosefe anauza abale akewo kuti: “Ndine Yosefe! Kodi bambo anga adakali ndi moyo?” Koma abale akewo sanathe kumuyankha chifukwa anali atawasokoneza maganizo. 4 Ndiyeno Yosefe anauza abale akewo kuti: “Sunthirani pafupi ndi ine.” Ndipo anasunthiradi pafupi ndi iye.
Kenako Yosefe anati: “Ndine mʼbale wanu uja Yosefe, amene munamugulitsa ku Iguputo.+ 5 Koma musadzimvere chisoni kapena kuimbana mlandu kuti munandigulitsa kuno, chifukwa Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti tikhalebe ndi moyo.+ 6 Chino ndi chaka chachiwiri cha njala padziko pano.+ Kutsogoloku kukubwera zaka zina 5 zimene anthu sadzalima kapena kukolola. 7 Koma Mulungu ananditumiza kuno, kuti anthu inu musatheretu+ padziko lapansi,* komanso kuti mukhalebe ndi moyo pokupulumutsani modabwitsa. 8 Choncho si inu amene munanditumiza kuno, koma ndi Mulungu woona. Anachita zimenezi kuti andiike kukhala nduna yaikulu ya* Farao, mbuye wa nyumba yake yonse ndiponso wolamulira wa dziko lonse la Iguputo.+
9 Bwererani kwa bambo anga msanga, ndipo mukawauze kuti, ‘Mwana wanu Yosefe wanena kuti: “Mulungu wandiika ine kukhala mbuye wa dziko lonse la Iguputo.+ Bwerani kuno kwa ine, musachedwe.+ 10 Mudzakhala mʼdziko la Goseni+ kuti mudzakhale pafupi ndi ine. Mubwere inuyo, ana anu, adzukulu anu, nkhosa zanu, ngʼombe zanu ndi zonse zimene muli nazo. 11 Kumeneko ndizidzakupatsani chakudya chifukwa kwatsala zaka 5 za njala.+ Mukapanda kuchita zimenezi, inuyo ndi amʼnyumba yanu komanso zonse zimene muli nazo muvutika ndi njala.”’ 12 Inuyo ndi mʼbale wangayu Benjamini, mukuona ndi maso anu kuti ndine amene ndikulankhula nanu.+ 13 Choncho, mukauze bambo anga za ulemerero wanga wonse ku Iguputo kuno ndi zonse zimene mwaona. Ndiye fulumirani mukatenge bambo anga nʼkubwera nawo kuno.”
14 Yosefe atatero, anakumbatira Benjamini mʼbale wake nʼkuyamba kulira. Nayenso Benjamini analira atakumbatira mʼbale wakeyo.+ 15 Kenako Yosefe anakisa abale ake onsewo nʼkumalira akuwakumbatira. Pambuyo pake, abale akewo analankhula naye.
16 Uthenga unafika kunyumba kwa Farao wakuti: “Abale ake a Yosefe abwera!” Farao ndi atumiki ake anasangalala atamva zimenezo. 17 Choncho Farao anauza Yosefe kuti: “Abale akowa uwauze kuti, ‘Chitani izi: Kwezani katundu panyama zanu, mupite kudziko la Kanani. 18 Mukatenge bambo anu ndi mabanja anu nʼkubwera nawo kuno kwa ine. Ndidzakupatsani zabwino zamʼdziko la Iguputo, ndipo mudzadya zinthu zochokera munthaka yachonde yamʼdzikoli.’+ 19 Uwauzenso kuti:+ ‘Chitani izi: Mutenge ngolo+ kuno ku Iguputo zoti mukatengeremo ana anu ndi akazi anu. Ngolo ina mukatengeremo bambo anu nʼkubwera kuno.+ 20 Musadandaule za katundu wanu,+ chifukwa zabwino za dziko lonse la Iguputo ndi zanu.’”
21 Ana a Isiraeli aja anachitadi zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga momwe Farao analamulira. Anawapatsanso chakudya cha pa ulendo. 22 Aliyense wa iwo anamupatsa chovala chatsopano, koma Benjamini anamupatsa zovala zatsopano 5, ndi ndalama zasiliva 300.+ 23 Kwa bambo ake anatumizako abulu 10 onyamula zinthu zabwino zochokera ku Iguputo, abulu aakazi 10 onyamula tirigu ndi chakudya chawo cha pa ulendo. 24 Atatero, anauza abale akewo kuti anyamuke. Pamene ankanyamuka anawauza kuti: “Musakanganetu mʼnjira.”+
25 Iwo anachoka ku Iguputo kuja nʼkukafika kudziko la Kanani, kwa Yakobo bambo awo. 26 Atafika, anauza bambo awo kuti: “Yosefe uja ali moyo, ndipo ndi wolamulira wa dziko lonse la Iguputo!”+ Koma Yakobo atamva zimenezo sanawayankhe chifukwa sanawakhulupirire.+ 27 Koma atamufotokozera zonse zimene Yosefe ananena, ndiponso ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti zidzamutenge, Yakobo bambo awo anayamba kusangalala. 28 Kenako Isiraeli anafuula kuti: “Basi, tsopano ndakhulupirira! Yosefe mwana wanga adakali ndi moyo! Ndipita ndikamuone ndisanafe!”+