Machitidwe a Atumwi
23 Paulo anayangʼanitsitsa Khoti Lalikulu la Ayudalo nʼkunena kuti: “Anthu inu, abale anga, ndachita zinthu popanda chikumbumtima changa kunditsutsa ngakhale pangʼono pamaso pa Mulungu+ mpaka lero.” 2 Hananiya mkulu wa ansembe atamva zimenezi, analamula anthu amene anaimirira pafupi naye kuti amʼmenye pakamwa. 3 Atatero, Paulo anamuuza kuti: “Uona, Mulungu akulanga, khoma lopaka laimu iwe. Wakhala pamenepo kuti undiweruze motsatira Chilamulo, ndiye ukuphwanyanso Chilamulocho polamula kuti andimenye?” 4 Anthu amene anaima naye pafupi anati: “Kodi ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?” 5 Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Chifukwa Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+
6 Paulo ataona kuti ena a iwo anali Asaduki ndipo ena anali Afarisi, anafuula mʼkhotimo kuti: “Anthu inu, abale anga, ine ndine Mfarisi,+ mwana wa Afarisi. Pano ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo chakuti akufa adzauka.” 7 Atanena zimenezi, Afarisi ndi Asaduki anayamba kukangana kwambiri, ndipo gululo linagawanika. 8 Chifukwa Asaduki amanena kuti munthu wakufa sangauke komanso kulibe angelo kapena cholengedwa chauzimu. Pomwe Afarisi amavomereza poyera kuti zonsezi zilipo.+ 9 Choncho panali chiphokoso, ndipo alembi ena a gulu la Afarisi anaimirira nʼkuyamba kutsutsa mwaukali kuti: “Sitikupeza chimene munthuyu walakwa. Koma ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye+ . . .” 10 Mkanganowo utakula kwambiri, mkulu wa asilikali anachita mantha kuti anthuwo amukhadzulakhadzula Paulo. Choncho analamula asilikali kuti apite akamuchotse pagululo nʼkubwera naye kumpanda wa asilikali.
11 Koma usiku wa tsiku lomwelo, Ambuye anaima pafupi ndi Paulo nʼkumuuza kuti: “Limba mtima.+ Chifukwa wandichitira umboni mokwanira ku Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.”+
12 Kutacha, Ayuda anakonza chiwembu nʼkulumbira pochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atapha Paulo. 13 Panali amuna oposa 40 amene anakonza chiwembu chochita kulumbirirachi. 14 Anthuwa anapita kwa ansembe aakulu ndi akulu kukanena kuti: “Ife talumbira pochita kudzitemberera kuti sitidya chilichonse mpaka titapha Paulo. 15 Tsopano inuyo ndi Khoti Lalikulu la Ayuda, muuze mkulu wa asilikali kuti abweretse Paulo kwa inu ngati kuti mukufuna kumvetsa bwino nkhani yake. Koma asanafike ife tidzamupha.”
16 Koma mwana wamwamuna wa mchemwali wake wa Paulo anamva kuti anthuwo akonza zokamudikirira panjira, ndipo anapita kumpanda wa asilikali nʼkukamuuza Paulo zimenezi. 17 Choncho Paulo anaitana mmodzi wa atsogoleri a asilikali nʼkumuuza kuti: “Mʼtenge mnyamatayu upite naye kwa mkulu wa asilikali chifukwa ali ndi mawu oti akamuuze.” 18 Choncho anamutengadi nʼkupita naye kwa mkulu wa asilikali ndipo ananena kuti: “Paulo, mkaidi uja, anandiitana nʼkundiuza kuti ndimubweretse mnyamatayu. Akuti ali ndi mawu oti akuuzeni.” 19 Mkulu wa asilikaliyo anamugwira dzanja mnyamatayo nʼkupita naye pambali ndipo anamufunsa kuti: “Ukufuna kundiuza chiyani?” 20 Iye anati: “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mupititse Paulo kubwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda, ngati kuti akufuna kumvetsa bwino mlandu wake.+ 21 Koma musalole kuti akunyengerereni, chifukwa amuna oposa 40 akufuna kudzamudikirira panjira. Anthu amenewa alumbira mochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atamupha.+ Moti panopa akonzeka, akungoyembekezera chilolezo chanu.” 22 Mkulu wa asilikaliyo anauza mnyamatayo kuti azipita atamulangiza kuti: “Usauze aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”
23 Ndiyeno anaitanitsa atsogoleri awiri a asilikali nʼkuwauza kuti: “Uzani asilikali 200 kuti akonzekere kuyenda ulendo wopita ku Kaisareya cha mʼma 9 koloko* usiku uno. Pakhalenso amuna 70 okwera pamahatchi* ndiponso asilikali 200 a mikondo. 24 Muwapatsenso mahatchi oti akwezepo Paulo kuti akafike kwa bwanamkubwa Felike ali wotetezeka.” 25 Ndiyeno iye analemba kalata yonena kuti:
26 “Ine Kalaudiyo Lusiya, ndikulembera inu Wolemekezeka Bwanamkubwa Felike: Landirani moni! 27 Munthu uyu anagwidwa ndi Ayuda ndipo anatsala pangʼono kumupha. Koma nthawi yomweyo ndinafika ndi gulu langa la asilikali nʼkumupulumutsa,+ chifukwa ndinamva kuti iyeyu ndi nzika ya Roma.+ 28 Ndiyeno pofuna kudziwa chimene anapalamula, ndinapita naye ku Khoti Lalikulu la Ayuda.+ 29 Kumeneko ndinapeza kuti akumuimba mlandu pa nkhani zokhudza Chilamulo chawo.+ Koma sanapezeke ndi mlandu uliwonse woyenera kuphedwa kapena kutsekeredwa mʼndende. 30 Komabe popeza ndadziwa chiwembu chimene amukonzera munthuyu,+ ndamutumiza kwa inu, ndipo ndalamula omuimba mlanduwo kuti adzanene mlandu wake pamaso panu.”
31 Choncho asilikaliwo anatenga Paulo+ usiku nʼkupita naye ku Antipatiri mogwirizana ndi zimene anawalamula. 32 Tsiku lotsatira anasiya amuna okwera pamahatchi aja kuti apitirire naye, koma iwo anabwerera kumpanda wa asilikali. 33 Amuna okwera pamahatchiwo anafika ku Kaisareya nʼkupereka kalata ija kwa bwanamkubwa ndipo anaperekanso Paulo. 34 Choncho bwanamkubwayo anawerenga kalatayo ndipo anafunsa chigawo chimene Paulo ankachokera. Anamva kuti ankachokera ku Kilikiya.+ 35 Ndiyeno anati: “Ndimvetsera mlandu wako wonse anthu okuimba mlanduwo akafika.”+ Ndipo analamula kuti amusunge mʼnyumba ya Mfumu Herode nʼkumamulondera.