Nehemiya
1 Awa ndi mawu a Nehemiya*+ mwana wa Hakaliya. Mʼmwezi wa Kisilevi,* mʼchaka cha 20, ine ndinali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.*+ 2 Pa nthawiyo Haneni,+ mmodzi wa abale anga, anabwera limodzi ndi amuna ena kuchokera ku Yuda. Ndinawafunsa mmene zinthu zinalili kwa Ayuda amene anathawa ku ukapolo+ komanso za Yerusalemu. 3 Iwo anandiyankha kuti: “Anthu amene anatsala mʼchigawo,* omwe anapulumuka ku ukapolo, ali pamavuto aakulu ndipo akunyozedwa.+ Nawonso mpanda wa Yerusalemu unagwa+ ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto.”+
4 Nditangomva mawu amenewa, ndinakhala pansi nʼkuyamba kulira ndipo ndinalira kwa masiku angapo, kusala kudya+ komanso kupemphera kwa Mulungu wakumwamba. 5 Ndinati: “Inu Yehova Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu komanso wochititsa mantha. Inu mumakwaniritsa pangano lanu ndipo mumasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu.+ 6 Chonde, tsegulani maso anu ndi kutchera khutu kuti mumve pemphero la ine mtumiki wanu limene ndikupemphera kwa inu lero. Masana ndi usiku+ ndikumapempherera atumiki anu, Aisiraeli. Pochita zimenezi ndikuvomereza machimo a Aisiraeli amene tinakuchimwirani. Tonse tinachimwa, ine limodzi ndi nyumba ya bambo anga.+ 7 Tachita zinthu zolakwika pamaso panu+ ndipo sitinasunge malamulo, malangizo ndi ziweruzo zimene munapatsa mtumiki wanu Mose.+
8 Chonde, kumbukirani mawu amene munauza* mtumiki wanu Mose kuti, ‘Mukadzachita zinthu mosakhulupirika, ndidzakumwazani pakati pa anthu a mitundu ina.+ 9 Koma mukadzabwerera kwa ine nʼkumatsatira malamulo anga, ngakhale anthu a mtundu wanu atamwazikira kumalekezero akumwamba, ndidzawasonkhanitsa+ kuchokera kumeneko nʼkuwabweretsa kumalo amene ndasankha kuti kukhale dzina langa.’+ 10 Iwo ndi atumiki anu komanso anthu anu amene munawawombola ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 11 Inu Yehova, chonde mvetserani pemphero la ine mtumiki wanu ndiponso pemphero la atumiki anu amene amaopa dzina lanu ndi mtima wonse. Chonde, ndithandizeni ine mtumiki wanu kuti zinthu zindiyendere bwino lero ndipo munthuyu andichitire chifundo.”+
Pa nthawiyi ndinali woperekera zakumwa kwa mfumu.+