FUNSO 6
Kodi Baibulo linaneneratu zinthu ziti zokhudza Mesiya?
ULOSI
“Iwe Betelehemu Efurata, . . . mwa iwe mudzatuluka munthu amene ndidzamusankhe kuti akhale wolamulira mu Isiraeli.”
KUKWANIRITSIDWA KWAKE
“Yesu atabadwa ku Betelehemu wa ku Yudeya, pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Herode, okhulupirira nyenyezi ochokera Kumʼmawa anabwera ku Yerusalemu.”
ULOSI
“Iwo akugawana zovala zanga, ndipo akuchita maere pa zovala zanga.”
KUKWANIRITSIDWA KWAKE
“Asilikaliwo atamukhomerera Yesu pamtengo, anatenga malaya ake akunja nʼkuwagawa zigawo 4. . . . Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anawombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi. Choncho iwo anakambirana kuti: ‘Malayawa tisawangʼambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.’ ”
ULOSI
“Amateteza mafupa onse a munthu wolungamayo. Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.”
KUKWANIRITSIDWA KWAKE
“Atafika pa Yesu, anapeza kuti wafa kale ndiye sanamuthyole miyendo.”
ULOSI
“Iye anabayidwa chifukwa cha zolakwa zathu.”
KUKWANIRITSIDWA KWAKE
“Mmodzi wa asilikaliwo anamubaya ndi mkondo munthiti ndipo nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi.”
ULOSI
“Iwo anandilipira ndalama 30 zasiliva.”
KUKWANIRITSIDWA KWAKE
“Kenako mmodzi wa ophunzira 12 aja, amene ankadziwika kuti Yudasi Isikariyoti, anapita kwa ansembe aakulu nʼkuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?” Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.”