“Monga Nyenyezi za Kumwamba”
“Ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” (Genesis 22:17) Chotero Mulungu analonjeza kholo Abrahamu. Nkhani ya posachedwapa ya chofalitsidwa cha Bible Review, ngakhale kuli tero, ikulozera ku lowoneka kukhala vuto ndi lemba limeneli.
Baibulo liri mwa sayansi lolondola m’kuyerekezera chiŵerengero cha nyenyezi m’mlengalenga ku mabiliyoni a mchenga wa m’nyanja. Komabe, kunena kuti nyenyezi zimafika ku chiŵerengero cha mabiliyoni chinadziŵika mwachiwonekere nthaŵi za kumbuyo. Inalongosola tero Bible Review: “Palibe kwenikweni unyinji woterowo wa nyenyezi m’mwamba zomwe zingawonedwe ndi maso osathandizidwa. Akatswiri a za m’mlengalenga akutiwuza ife kuti popanda zinthu zina zonga zokuzira zinthu, tingakhoze kokha kuwona nyenyezi pakati pa 2,000 ndi 4,000, ngakhale m’usiku wopanda mitambo.” The World Book Encyclopedia yalongosola kuti “chifupifupi nyenyezi 6,000 zimawala mowalikira kwambiri kuti ziwonedwe popanda zokuzira zinthu.”
Chotero, ndimotani, mmene wina amalongosolera kulondola kodabwitsa kwa Baibulo m’kupanga kuyerekeza kumeneku? Kulongosola kumodzi kukakhala kwakuti Baibulo liri “lowuziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Nkhani mu Bible Review, ngakhale kuli tero, imapita ku utali wokulira kukulitsa mathedwe amenewa mwakulingalira kuti mwinamwake Abrahamu anali katswiri wodziŵa za m’mlengalenga! Kalongosoledwe komvekera kameneka kanatsatiridwa ndi funso lakuti: “Kodi akale angakhale anali ndi zokuzira zinthu zomwe zinavumbula nyenyezi zomwe maso opanda kanthu sakakhoza kuwona?” Kuchirikiza nthanthi imeneyi, nkhaniyo inagwira mawu umboni wa zonyezimira zopezedwa mu Nineve ndi malo ena akale zomwe zikakhoza kutumikira monga magalasi akale.
Komabe, umboni wakuti anthu akale anagwiritsira ntchito magalasi oterowo kaamba ka kuwonera nyenyezi kulibeko. Ndipo ngakhale ngati zokuzira zinthu zakale zinalipo, kodi ndi umboni wotani umene ulipo wakuti Abrahamu kapena mlembi wa Genesis anali ndi chimodzi? Kwenikweni, lonjezo la Mulungu kwa Abrahamu liri kokha chimodzi cha zitsanzo zambiri za kulondola kwa usayansi kwa Baibulo. Iko mwachiwonekere kunali popanda thandizo la chokuzira zinthu pamene m’neneri Yeremiya anasimba kawonedwe kolondola kofananako: ‘Khamu lakuthambo silingathe kuŵerengedwa, ndiponso mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa.’—Yeremiya 33:22.
[Mawu a Chithunzi patsamba 23]
NASA photos